Yobu 10:1-22

  • Yankho la Yobu likupitirira (1-22)

    • ‘Nʼchifukwa chiyani Mulungu akulimbana nane?’ (2)

    • Kusiyana kwa Mulungu ndi Yobu (4-12)

    • ‘Ndipumeko pangʼono’ (20)

10  “Moyo wanga ndikunyansidwa nawo.+ Ndinena madandaulo anga mwamphamvu. Ndilankhula mopwetekedwa mtima.*  2  Ndimuuza Mulungu kuti: ‘Musanene kuti ndine wolakwa. Ndiuzeni chifukwa chake mukulimbana nane.  3  Kodi mukupindula chilichonse mukamandizunza,Mukamanyoza ntchito ya manja anu,+Pamene mukugwirizana ndi zolinga za oipa?  4  Kodi maso anu ali ngati a munthu,Kapena kodi mumaona ngati mmene munthu amaonera?  5  Kodi masiku anu ali ngati masiku a anthu,Kapena kodi zaka zanu zili ngati za munthu,+  6  Kuti muzifufuza zolakwa zangaKomanso kuti muzifunafuna tchimo langa?+  7  Inu mukudziwa kuti ndine wosalakwa,+Ndipo palibe amene angandipulumutse mʼmanja mwanu.+  8  Manja anu ndi amene anandiumba ndiponso kundipanga,+Koma tsopano mukufuna kundiwonongeratu.  9  Chonde kumbukirani kuti munandiumba ndi dongo,+Koma tsopano mukufuna kundibwezera kufumbi.+ 10  Kodi simunandikhuthule ngati mkakaNʼkundichititsa kuti ndiundane ngati tchizi?* 11  Munandiveka khungu ndiponso mnofu,Ndipo munandiluka ndi mafupa komanso mitsempha.+ 12  Mwandipatsa moyo komanso mwandisonyeza chikondi chokhulupirika,Ndipo mumanditeteza* pondisamalira.+ 13  Koma inu mukufuna kuchita zinthu zimenezi mwachinsinsi.* Ndikudziwa kuti zimenezi zachokera kwa inu. 14  Ndikanachimwa mukanandiona,+Ndipo simukanandikhululukira zolakwa zanga. 15  Ngati ndili wolakwa, tsoka kwa ine! Ndipo ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingadzutse mutu wanga,+Chifukwa ndili ndi manyazi kwambiri ndipo ndikuvutika.+ 16  Ndikakweza mutu wanga, mumandisaka ngati mmene umachitira mkango+Ndipo mumasonyezanso mphamvu zanu polimbana nane. 17  Mumabweretsa mboni zatsopano kuti zinditsutseNdipo mumawonjezera mkwiyo wanu pa ine,Moti mavuto anga akungotsatizanatsatizana. 18  Ndiye nʼchifukwa chiyani munanditulutsa mʼmimba mwa mayi anga?+ Zikanakhala bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione. 19  Zikanakhala ngati sindinakhaleko.Ndikanangochokera mʼmimba nʼkupita kumanda.’ 20  Kodi si paja masiku a moyo wanga atsala ochepa?+ Iye andisiye,Asiye kundiyangʼanitsitsa kuti ndipumuleko pangʼono*+ 21  Ndisanapite kumalo amene sindidzabwerako,+Kudziko lamdima wandiweyani,*+ 22  Kudziko lamdima waukulu,Dziko lamdima wandiweyani komanso lachisokonezo,Kumene ngakhale kuwala kumafanana ndi mdima.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.”
Tchizi ndi chakudya chopangidwa kuchokera ku mkaka.
Kapena kuti, “mumateteza moyo wanga; mumateteza mpweya wanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo zinthu zimenezi mwazibisa mumtima mwanu.”
Kapena kuti, “ndisangalaleko pangʼono.”
Kapena kuti, “Kudziko lamdima komanso mthunzi wa imfa.”