Yobu 12:1-25
12 Kenako Yobu anayankha kuti:
2 “Zoonadi, anthu inu mukudziwa zinthu zambiri,*Ndipo nzeru zidzathera limodzi ndi inu.
3 Koma inenso ndine wozindikira* ngati inuyo.
Si ine munthu wamba poyerekezera ndi inu.
Ndi ndani amene sakudziwa zimenezi?
4 Ine ndakhala chinthu choseketsa kwa anzanga,+Ndakhala munthu amene akuitana Mulungu kuti amuyankhe.+
Munthu wolungama komanso wosalakwa wakhala choseketsa.
5 Amene zinthu zikuwayendera bwino amanyoza amene akumana ndi tsoka,Iwo amaganiza kuti limagwera anthu okhawo amene akukumana kale ndi mavuto.*
6 Anthu akuba amakhala mwamtendere mʼmatenti awo,+Amene amakwiyitsa Mulungu amakhala otetezeka,+Anthu amene mulungu wawo ali mʼmanja mwawo.
7 Koma funsa nyama ndipo zidzakuphunzitsa.Komanso mbalame zamumlengalenga, ndipo zidzakuuza.
8 Kapena chita chidwi* ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa,Komanso nsomba zamʼnyanja ndipo zidzakuuza.
9 Kodi ndi ndani pa zonsezi amene sakudziwaKuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi?
10 Moyo wa chilichonse uli mʼdzanja lake,Ndiponso mzimu* wa munthu aliyense.+
11 Kodi si paja khutu limasiyanitsa mawuNgati mmene lilime limasiyanitsira* kakomedwe ka chakudya?+
12 Kodi si paja okalamba amakhala ndi nzeru,+Ndipo amene akhala moyo wautali si paja amamvetsa zinthu?
13 Mulungu ali ndi nzeru komanso mphamvu.+Iye amamvetsa zinthu ndipo adzakwaniritsa cholinga chake.+
14 Iye akagwetsa chinthu, sichingamangidwenso,+Zimene iye watseka, palibe munthu amene angatsegule.
15 Akaletsa mvula, chilichonse chimauma,+Akalola kuti ibwere, madzi amasefukira padziko lapansi.+
16 Iye ali ndi mphamvu komanso nzeru zopindulitsa.+Ali ndi mphamvu pa munthu amene akusochera ndi amene akusocheretsa ena.
17 Iye amachititsa kuti alangizi ayende opanda nsapato,*Ndipo amapusitsa oweruza.+
18 Amamasula zingwe zimene mafumu amangira anthu,+Ndipo amawamanga lamba mʼchiuno mwawo.
19 Amachititsa kuti ansembe ayende opanda nsapato,+Ndipo amachotsa paudindo olamulira amphamvu.+
20 Alangizi okhulupirika amawasowetsa chonena,Ndipo amachotsa kuzindikira kwa amuna achikulire,*
21 Iye amachititsa manyazi anthu olemekezeka,+Ndipo amachititsa anthu amphamvu kuti akhale ofooka.*
22 Amaulula zinthu zozama zimene zili mumdima,+Ndipo amabweretsa kuwala mumdima wandiweyani.
23 Amachititsa mitundu kuti ikhale yamphamvu nʼcholinga choti aiwononge.Amakulitsa mitundu kuti aipititse ku ukapolo.
24 Amachotsa nzeru za atsogoleri* a anthuwo,Ndipo amawachititsa kuti azingoyendayenda mʼchipululu mmene mulibe njira.+
25 Iwo amafufuza mumdima+ mmene mulibe kuwala,Iye amawachititsa kuti aziyendayenda ngati anthu oledzera.”+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu inu ndinu anthu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “inenso ndili ndi mtima.”
^ Kapena kuti, “anthu okhawo amene mapazi awo aterereka.”
^ Mabaibulo ena amati, “lankhula.”
^ Kapena kuti, “mpweya.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼkamwa mumasiyanitsira.”
^ Kapena kuti, “ayende atavulidwa chilichonse.”
^ Kapena kuti, “kwa akulu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo amakhwepetsa lamba wa anthu amphamvu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Amachotsa mtima wa atsogoleri.”