Yobu 18:1-21
18 Bilidadi+ wa ku Shuwa anayankha kuti:
2 “Kodi usiya nthawi yanji kulankhula choncho?
Sonyeza kuti ndiwe wozindikira kuti nafenso tilankhule.
3 Nʼchifukwa chiyani ukutiona ngati zinyama+Ndiponso ngati anthu opusa?*
4 Ngakhale utadzikhadzulakhadzula chifukwa choti wakwiya,Kodi dziko lapansi lingasiyidwe chifukwa cha iwe?Kapena kodi thanthwe lingasunthe pamalo ake?
5 Inde, kuwala kwa woipa kudzazimitsidwa,Ndipo malawi a moto wake sadzawala.+
6 Kuwala kwa mutenti yake kudzazima,Ndipo nyale imene ili mutenti yake idzazimitsidwa.
7 Adzakhala alibe mphamvu zoti nʼkuyendera,Ndipo mapulani ake adzamubweretsera mavuto.+
8 Mapazi ake adzamugwetsera mu ukonde,Ndipo adzayenda mʼzingwe za ukondewo.
9 Msampha udzamugwira chidendene.Khwekhwe lidzamukola.+
10 Chingwe chabisidwa pansi kuti chimukole,Ndipo msampha uli panjira yake.
11 Zoopsa zimamuchititsa mantha paliponse,+Ndipo zimamuthamangitsa zili naye pafupi kwambiri.
12 Mphamvu zake zimachepa,Ndipo tsoka+ lidzamuchititsa kuti ayende modzandira.*
13 Khungu lake ladyeka.Matenda oopsa kwambiri agwira* manja ndi miyendo yake.
14 Iye adzachotsedwa mʼmalo otetezeka amutenti yake,+Ndipo adzamupititsa kwa mfumu ya zinthu zoopsa.*
15 Anthu achilendo adzakhala* mutenti yake.Sulufule adzamwazidwa panyumba yake.+
16 Pansi, mizu yake idzauma,Ndipo pamwamba, nthambi zake zidzafota.
17 Anthu sadzamukumbukiranso padziko lapansi,Ndipo mumsewu dzina lake silidzadziwika.*
18 Adzamuchotsa powala nʼkumupititsa kumdimaNdipo adzamuthamangitsa padziko lapansi.
19 Iye sadzasiya ana kapena mbadwa pakati pa anthu ake,Ndipo sipadzakhala wopulumuka pamalo amene iye akukhala.*
20 Tsiku la tsoka lake likadzafika, anthu a Kumadzulo adzachita mantha kwambiri,Ndipo anthu a Kumʼmawa adzagwidwa ndi mantha aakulu.
21 Izi nʼzimene zimachitikira matenti a munthu wochita zoipa,Komanso malo a munthu amene sadziwa Mulungu.”
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “anthu odetsedwa.”
^ Kapena kuti, “motsimphina.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mwana woyamba kubadwa wa imfa wagwira.”
^ Kapena kuti, “adzamupititsa ku imfa yowawa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Chinthu chomwe si chake chidzakhala.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzakhala ndi dzina.”
^ Kapena kuti, “pamalo amene akukhala monga mlendo.”