Yobu 28:1-28
28 “Pali malo amene anthu amakumba siliva,Ndiponso malo amene amakumba golide yemwe amamuyenga.+
2 Chitsulo chimatengedwa munthaka,Ndipo kopa* amatengedwa* kuchokera mʼmiyala.+
3 Munthu amagonjetsa mdima,Amafufuza mpaka pamapeto mumdima wandiweyani,Kufunafuna miyala ya mtengo wapatali.
4 Amakumba mgodi kutali ndi kumene anthu amakhala,Kumalo oiwalika, kutali ndi kumene anthu amayenda.Anthu ena amatsikira pansi nʼkumagwira ntchito akulendewera.
5 Padziko lapansi pamamera chakudya,Koma pansi pake pasintha ngati kuti pawonongedwa ndi moto.*
6 Mʼmiyala yake mumapezeka miyala ya safiro,Ndipo mufumbi lake mumapezeka golide.
7 Mbalame yodya nyama sikudziwa njira yopita kumeneko,Ndipo diso la mphamba wakuda silinaionepo.
8 Zilombo zamphamvu sizinapondemo,Mkango wamphamvu sunasakemo nyama.
9 Munthu amaswa mwala wolimba ndi manja ake,Amagwetsa mapiri kuyambira pansi penipeni.
10 Amapanga ngalande zamadzi+ pathanthwe,Ndipo maso ake amaona chinthu chilichonse chamtengo wapatali.
11 Kumene mitsinje imayambira, amakumbako madamu,Ndipo chinthu chobisika amachibweretsa poyera.
12 Koma kodi nzeru zingapezeke kuti?+Ndipo kumvetsa zinthu kumachokera kuti?+
13 Palibe munthu amene angadziwe mtengo wake,+Ndipo nzeru sizingapezeke kulikonse padziko lapansi.
14 Madzi akuya anena kuti,‘Sizili mwa ine.’
Ndipo nyanja yanena kuti, ‘Sizili ndi ine.’+
15 Sizingagulidwe ndi golide woyenga bwino,Ndipo munthu sangapereke siliva kuti apeze nzeru.+
16 Sangazigule ndi golide wa ku Ofiri,+Kapena mwala wosowa wa onekisi ndi wa safiro.
17 Nzeru sitingaziyerekezere ndi golide komanso galasi,Ndipo sitingazisinthanitse ndi mbale ya golide woyenga bwino.+
18 Miyala yamtengo wapatali ya korali ndi kulusitalo sitingaiyerekezere nʼkomwe ndi nzeru.+Ndipo thumba lodzaza ndi nzeru ndi lamtengo wapatali kuposa thumba lodzaza ndi ngale.
19 Sitingaziyerekezere ndi miyala ya topazi+ ya ku Kusi,Ngakhale golide woyenga bwino sangagulire nzeru.
20 Koma kodi nzeru zimachokera kuti,Ndipo kumvetsa zinthu kumachokera kuti?+
21 Zabisika pamaso pa chamoyo chilichonse,+Ndipo nʼzobisika kwa mbalame zamumlengalenga.
22 Chiwonongeko ndi imfa zanena kuti,‘Makutu athu angomva lipoti chabe lokhudza nzeruzo.’
23 Mulungu yekha ndi amene amadziwa njira yozipezera,Iye yekha ndi amene amadziwa kumene zimakhala.+
24 Chifukwa amayangʼana kumapeto kwa dziko lapansi,Ndipo amaona chilichonse chimene chili pansi pa thambo.+
25 Pamene mphepo ankaipatsa mphamvu,*+Komanso pamene ankayeza kuchuluka kwa madzi,+
26 Pamene mvula ankaipangira lamulo,+Komanso pamene ankapanga njira ya mtambo wamvula yamabingu,+
27 Pa nthawi imeneyo iye anaona nzeru pa ntchito imene anagwira nʼkuyamba kuzifotokoza.Iye anazikhazikitsa nʼkuziyesa.
28 Ndiyeno anauza munthu kuti:
‘Tamvera, kuopa Yehova ndi nzeru,+Ndipo kupewa zoipa ndiko kumvetsa zinthu.’”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mkuwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amakhuthulidwa.”
^ Zikuoneka kuti apa akunena ntchito za mʼmigodi.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kulemera.”