Yobu 31:1-40

  • Yobu ananena kuti adzapitirizabe kukhala wokhulupirika (1-40)

    • “Pangano ndi maso anga” (1)

    • Anapempha kuti Mulungu amuyeze pasikelo (6)

    • Sanali wachigololo (9-12)

    • Sankakonda ndalama (24, 25)

    • Sankalambira mafano (26-28)

31  “Ndachita pangano ndi maso anga.+ Choncho ndingayangʼanitsitse bwanji namwali momusilira?+  2  Kodi ndingalandire gawo lotani kuchokera kwa Mulungu kumwamba?Kodi cholowa chochokera kwa Wamphamvuyonse mʼmwamba chingakhale chiyani?  3  Kodi si paja wochita zoipa amayembekezera kukumana ndi mavuto,Ndipo ochita zoipa tsoka limawagwera?+  4  Kodi iye saona njira zanga,+Ndi kuwerenga masitepe anga onse?  5  Kodi ndinayamba ndanenapo zabodza? Kodi ndinayamba ndachitirapo aliyense zachinyengo?+  6  Mulungu andiyeze pamasikelo olondola,+Akatero adzaona kuti ndine wokhulupirika.+  7  Ngati phazi langa lapatuka kusiya njira,+Kapena ngati mtima wanga watsatira zimene maso anga aona,Kapenanso ngati manja anga adetsedwa,+  8  Ine ndidzale mbewu wina nʼkudya,+Ndipo zimene ndinadzala zidzazulidwe.*  9  Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,+Ndipo ndadikirira+ pakhomo la nyumba ya mnzanga, 10  Mkazi wanga aperere ufa mwamuna wina,Ndipo amuna ena agone naye.+ 11  Chifukwa limenelo lingakhale khalidwe lochititsa manyazi,Chingakhale cholakwa chimene oweruza akuyenera kundipatsira chilango.+ 12  Ungakhale moto umene unganyeketse komanso kuwononga zinthu,*+Ungapsereze ngakhale mizu ya mbewu* zanga zonse. 13  Ngati ndinalephera kuweruza mwachilungamo kapolo wanga wamwamuna kapena wamkaziPamene anali ndi mlandu ndi ine, 14  Ndiye ndingatani Mulungu akamandiweruza?* Kodi ndingamuyankhe chiyani atandifunsa?+ 15  Kodi amene anandipanga mʼmimba si amene anapanganso iwowo?+ Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe tisanabadwe?*+ 16  Ngati ndinakana kupatsa osauka zimene ankafuna,+Kapena kuchititsa kuti mkazi wamasiye amve chisoni,*+ 17  Ngati ndinkadya ndekha chakudya changa,Osagawirako ana amasiye,+ 18  (Chifukwa kuyambira ndili mnyamata, ana amasiye akula ndi ine ngati bambo awo,Ndipo kuyambira ndili mwana* ndakhala ndikuthandiza akazi amasiye.) 19  Ngati ndinkaona munthu akuzunzika ndi mphepo chifukwa chosowa chovala,Kapena munthu wosauka akusowa chofunda,+ 20  Ngati iye sanandidalitse*+Pamene ankamva kutentha atafunda chofunda cha ubweya wa nkhosa zanga, 21  Ngati ndinaopseza mwana wamasiye ndi chibakera+Pamene ankafuna kuti ndimuthandize pageti la mzinda,+ 22  Mkono wanga ugwe* kuchoka mʼmalo mwake,Ndipo mkono wanga uthyoke pachigongono.* 23  Chifukwa ine ndinkaopa tsoka lochokera kwa Mulungu,Ndipo ulemerero wake unkandichititsa mantha. 24  Ngati ndikudalira golide,Kapena kuuza golide woyenga bwino kuti, ‘Ndimadalira iwe.’+ 25  Ngati ndinkasangalala chifukwa chakuti ndinali ndi chuma chochuluka,+Chifukwa cha zinthu zambiri zimene ndinapeza,+ 26  Ngati ndinaona dzuwa likuwala*Kapena mwezi ukuyenda mwaulemerero,+ 27  Ngati mtima wanga unakopeka mwachinsinsi,Milomo yanga nʼkukisa dzanja langa pozilambira,+ 28  Chimenecho chikanakhala cholakwa chimene oweruza akuyenera kundipatsira chilango,Chifukwa ndikanakhala nditakana Mulungu woona wakumwamba. 29  Kodi ndinayamba ndasangalalapo chifukwa cha kuwonongedwa kwa mdani wanga,+Kapena kunyadira chifukwa chakuti zoipa zamuchitikira? 30  Ine sindinalole kuti mʼkamwa mwanga muchimwe,Popempha mochita kulumbira kuti afe.+ 31  Kodi amuna amutenti yanga sananene kuti,‘Ndi ndani amene angabwere ndi munthu amene sanakhute chakudya chake?’*+ 32  Palibe mlendo amene ankagona panja usiku.+Khomo langa linali lotsegula kwa anthu apaulendo. 33  Kodi ndinayamba ndayesapo kubisa zolakwa zanga, ngati anthu ena,+Pobisa machimo anga mʼthumba la chovala changa? 34  Kodi ndinachitapo mantha ndi zimene gulu la anthu lingachite,Kapena ndinayamba ndaopa mawu onyoza a mabanja ena,Nʼkundichititsa kukhala chete komanso kuopa kutuluka panja? 35  Zikanakhala bwino wina akanandimvetsera.+ Ndikanasainira dzina langa pa zimene ndanena.* Wamphamvuyonse andiyankhe.+ Zikanakhala bwino munthu amene akundiimba mlandu akanalemba milandu yanga papepala. 36  Ndikanalinyamula paphewa langa.Ndipo ndikanalikulungiza kumutu kwanga ngati chisoti. 37  Ndikanamufotokozera mwatsatanetsatane chilichonse chimene ndinachita.Ndikanapita kwa iye molimba mtima ngati kalonga. 38  Ngati munda wanga ukanalira modandaula chifukwa cha ineNdipo ngati mizere yake ikanalirira pamodzi, 39  Ngati ndadya zipatso zake osalipira,+Kapena ngati ndachititsa eniake a malowo kuti ataye mtima,+ 40  Minga zimere mʼmunda mwanga mʼmalo mwa tiriguNdipo mʼmalo mwa balere pamere zitsamba zonunkha.” Mawu a Yobu athera pamenepa.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mbadwa zanga zidzazulidwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “umene ungadye mpaka kuwonongeratu zinthu.”
Kapena kuti, “Ungazule mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akaimilira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmimba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchititsa maso a mkazi wamasiye kufooka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndili mʼmimba mwa mayi anga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chiuno chake sichinandidalitse.”
Kapena kuti, “Fupa lapaphewa langa ligwe.”
Kapena kuti, “kuchoka mʼmalomwake; pafupa lakumtunda kwake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinaona kuwala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyama yake.”
Kapena kuti, “Siginecha yanga ndi imeneyi.”