Yobu 6:1-30

  • Yankho la Yobu (1-30)

    • Ananena kuti akuyenera kudandaula (2-6)

    • Anthu amene ankamutonthoza anali achinyengo (15-18)

    • “Munthu akamanena zoona, sizipweteka” (25)

6  Ndiyeno Yobu anayankha kuti:  2  “Zikanakhala bwino mavuto+ anga onse akanayezedwa kulemera kwake,Nʼkuikidwa pasikelo limodzi ndi masautso anga.  3  Chifukwa panopa akulemera kuposa mchenga wamʼnyanja. Nʼchifukwa chake ndalankhula mosaganiza bwino.*+  4  Chifukwa mivi ya Wamphamvuyonse yandilasa,Ndipo ine ndikumwa poizoni wa miviyo.+Mulungu akundiukira ndipo ndikuchita mantha kwambiri.  5  Kodi bulu wamʼtchire+ amalira ndi njala ali ndi msipu?Kapena kodi ngʼombe yamphongo imalira ili ndi chakudya?  6  Kodi chakudya chosakoma chingadyedwe chopanda mchere?Kapena kodi utomoni wa zomera umakoma?  7  Ndakana kukhudza zinthu zimenezi. Zili ngati chakudya chowonongeka.  8  Zikanakhala bwino zimene ndapempha zikanachitika,Ndiponso Mulungu akanandipatsa zimene ndikufuna.  9  Zikanakhala bwino Mulungu akanati angondiphwanya,Akanati atambasule dzanja lake nʼkundipha.+ 10  Ngakhale zimenezo, zikanatha kunditonthoza.Ndikanadumpha ndi chisangalalo ngakhale kuti ndikumva ululu wosaneneka,Chifukwa sindinakane mawu a Woyerayo.+ 11  Kodi ndili ndi mphamvu kuti ndipitirize kudikira?+ Ndipo kodi ndili ndi chiyembekezo chilichonse kuti ndipitirizebe kukhala ndi moyo?* 12  Kodi mphamvu zanga ndi zofanana ndi za thanthwe? Kapena kodi mnofu wanga ndi wopangidwa ndi kopa?* 13  Kodi pali chimene ndingachite kuti ndidzithandize,Pamene zinthu zonse zimene zinkandithandiza zachotsedwa kwa ine? 14  Aliyense amene sasonyeza mnzake chikondi chokhulupirika,+Adzasiyanso kuopa Wamphamvuyonse.+ 15  Abale anga enieni akhala osadalirika+ ngati mtsinje umene umayenda madzi nthawi ya mvula yokha,Umene umauma mvula ikatha. 16  Iwo ali ngati mitsinje imene imakhala ndi madzi akuda chifukwa cha matope,Amene amabwera madzi oundana akasungunuka. 17  Koma pakapita nthawi imakhala yopanda madzi ndipo imatha.Kukatentha, imauma. 18  Njira zake ndi zokhotakhota.Mitsinjeyo imapita kuchipululu kenako nʼkuuma. 19  Magulu a anthu amalonda a ku Tema+ amaifunafuna,Anthu apaulendo a ku Sheba*+ amaidikirira. 20  Amachita manyazi chifukwa amakhulupirira kuti apeza madzi,Koma akafikapo amakhumudwa. 21  Mofanana ndi zimenezi, ndi mmene inu mulili kwa ine.+Mwaona kuopsa kwa mavuto amene ndakumana nawo ndipo mwachita mantha.+ 22  Kodi ndanena kuti, ‘Ndipatseni kanthu,’ Kapena kodi ndapempha kuti mundiperekere mphatso kuchokera pa chuma chanu? 23  Kodi ndapempha kuti mundipulumutse mʼmanja mwa mdani,Kapena kuti mundilanditse* mʼmanja mwa anthu ankhanza? 24  Ndilangizeni, ndipo ine ndikhala chete.+Ndithandizeni kuti ndimvetse zimene ndalakwitsa. 25  Munthu akamanena zoona, sizipweteka.+ Koma kodi kudzudzula kwanu kuli ndi phindu lanji?+ 26  Kodi mwapangana kuti mudzudzule mawu anga,Mawu a munthu amene wasokonezeka maganizo,+ omwe amatengedwa ndi mphepo? 27  Inutu mukhoza kuchita maere kuti mutenge mwana wamasiye,+Ndipo mnzanu mukhoza kumugulitsa.+ 28  Tsopano tembenukani ndipo mundiyangʼane,Chifukwa sindingakunamizeni. 29  Chonde ganizirani mofatsa, musandiweruze molakwa.Ndithu ganizirani mofatsa, chifukwatu ine ndikadali wolungama. 30  Kodi lilime langa likulankhula zinthu zopanda chilungamo? Kodi mʼkamwa mwanga simuzindikira kuti chinachake chalakwika?”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zopanda pake; zopanda nzeru.”
Kapena kuti, “kuti nditalikitse moyo wanga.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
Kapena kuti, “Gulu la Asabeya apaulendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mundiwombole.”