Yobu 9:1-35
9 Yobu anayankha kuti:
2 “Ndikudziwa ndithu kuti zili choncho.
Koma kodi munthu anganene bwanji kuti ndi wosalakwa pamaso pa Mulungu?+
3 Ngati munthu akufuna kutsutsana ndi Mulungu,*+Munthuyo sangathe kuyankha funso ndi limodzi lomwe pamafunso ake 1,000.
4 Iye ali ndi mtima wanzeru ndiponso mphamvu zambiri.+
Ndani angatsutsane naye koma osavulala?+
5 Iye amasuntha* mapiri popanda aliyense kudziwa.Amawagubuduza atakwiya.
6 Amagwedeza dziko lapansi nʼkulisuntha pamalo ake,Moti zipilala zake zimagwedera.+
7 Amalamula dzuwa kuti lisawaleNdipo amaphimba kuwala kwa nyenyezi.+
8 Iye amatambasula kumwamba yekha,+Ndipo amayenda pamafunde ataliatali a mʼnyanja.+
9 Anapanga gulu la nyenyezi la Asi, la Kesili ndi la Kima,+Komanso gulu la nyenyezi za kumʼmwera.
10 Amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,+Zinthu zodabwitsa zimene ndi zosatheka kuziwerenga.+
11 Iye amadutsa pafupi ndi ine koma sinditha kumuona,Amandidutsa koma ine osamuzindikira.
12 Iye akalanda chinthu, ndani angalimbane naye?
Ndani angamufunse kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+
13 Mulungu sadzabweza mkwiyo wake.+Ngakhale anthu othandiza Rahabi*+ adzamugwadira.
14 Nʼchifukwa chake ndikamamuyankha,Ndiyenera kusankha bwino mawu anga.
15 Ngakhale nditakhala kuti ndikunena zoona, sindingamuyankhe.+
Koma ndingachonderere woweruza wanga kuti andichitire chifundo.
16 Kodi nditamuitana, angandiyankhe?
Sindikukhulupirira kuti angandimvetsere.
17 Chifukwa iye wandivulaza ndi mavuto angati mphepo yamkuntho,Ndipo wachulukitsa mabala anga popanda chifukwa.+
18 Sakulola kuti ndikokeko mpweya,Ndipo akungopitiriza kuwonjezera mavuto anga.
19 Pa nkhani yokhala ndi mphamvu, iye ndi wamphamvu kwambiri.+
Pa nkhani yochita zinthu mwachilungamo, iye amanena kuti: ‘Ndi ndani angandiimbe mlandu?’*
20 Ngakhale ndikanapezeka kuti ndine wosalakwa, pakamwa panga pakanandiweruza kuti ndine wolakwa.Ngakhale nditakhala wokhulupirika,* adzandipezabe ndi mlandu.*
21 Ngakhale nditakhala wokhulupirika,* sindikudziwa zimene zingandichitikire,Moyo wangawu sindikuufunanso.*
22 Zonsezi mfundo yake ndi imodzi. Nʼchifukwa chake ndikunena kuti,‘Iye amawononga onse, osalakwa* komanso oipa.’
23 Anthu atafa mwadzidzidzi ndi madzi osefukira,Iye angaseke anthu osalakwa akuvutika.
24 Dziko lapansi laperekedwa mʼmanja mwa anthu oipa.+Iye amaphimba maso a oweruza* a dzikolo.
Ngati si iyeyo, ndiye ndi ndani?
25 Panopa masiku anga akufulumira kwambiri kuposa munthu wothamanga.+Iwo akuthawa asanaone zabwino.
26 Amayenda mofulumira ngati ngalawa za bango,Ngati ziwombankhanga zimene zimambwandira nyama yoti zidye.
27 Ngati nditanena kuti, ‘Ndiiwala kudandaula kwanga,Ndisintha maonekedwe a nkhope yanga nʼkukhala wosangalala,’
28 Ndingachitebe mantha chifukwa cha zopweteka zanga zonse,+Ndipo ndikudziwa kuti simungandipeze kuti ndine wosalakwa.
29 Ndingapezekebe kuti ndine wolakwa.*
Ndiye ndivutikirenji pachabe?+
30 Nditati ndisambe mʼmadzi oyera,*Komanso kusamba mʼmanja ndi sopo,+
31 Inuyo mungandiviike mʼdzenje la matope,Moti ngakhale zovala zanga zomwe zinganyansidwe nane.
32 Chifukwa iye si munthu ngati ine kuti ndingamuyankhe,Kapena kuti titengerane kukhoti.+
33 Palibe munthu woti agamule mlandu wathu,*Amene angakhale woweruza wathu.*
34 Ngati iye akanasiya kundimenya,*Komanso kundiopseza ndi zinthu zake zochititsa mantha,+
35 Ndikanalankhula naye mopanda mantha,Chifukwa ine sindiopa kulankhula.”
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “akufuna kutengera Mulungu kukhoti.”
^ Kapena kuti, “Iye amachotsa.”
^ Nʼkutheka kuti chimenechi ndi chilombo choopsa cha mʼnyanja.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndi ndani angandisumire?”
^ Kapena kuti, “Ngakhale nditakhala wosalakwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzapezabe kuti ndine wokhotakhota.”
^ Kapena kuti, “Ngakhale nditakhala wosalakwa.”
^ Kapena kuti, “ndikuunyoza; ndikuukana.”
^ Kapena kuti, “okhulupirika.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nkhope za oweruza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “woipa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmadzi achipale chofewa.”
^ Kapena kuti, “Palibe mʼkhalapakati pa mlandu wathu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Amene angaike dzanja lake patonsefe.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngati iye akanachotsa ndodo yake pa ine.”