Wolembedwa ndi Yohane 13:1-38
13 Tsopano Yesu anadziwiratu chikondwerero cha Pasika chisanafike kuti nthawi yake yochoka mʼdzikoli kupita kwa Atate+ yakwana.+ Ndipo popeza kuti ankakonda otsatira akewo amene anali mʼdzikoli, anawakonda mpaka pamapeto a moyo wake.+
2 Chakudya chamadzulo chinali chili mkati ndipo Mdyerekezi anali ataika kale maganizo ofuna kupereka Yesu+ mumtima mwa Yudasi Isikariyoti,+ mwana wa Simoni.
3 Yesu ankadziwa kuti Atate anapereka zinthu zonse mʼmanja mwake komanso kuti anabwera kuchokera kwa Mulungu ndiponso kuti ankapita kwa Mulungu.+
4 Choncho anaimirira pa chakudya chamadzulocho nʼkuvula malaya ake akunja. Kenako anatenga thaulo nʼkulimanga mʼchiuno mwake.+
5 Atatero anathira madzi mʼbeseni nʼkuyamba kusambitsa mapazi a ophunzirawo komanso kuwapukuta ndi thaulo limene anamanga mʼchiuno lija.
6 Kenako anafika pa Simoni Petulo. Koma Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, inuyo mukufuna musambitse mapazi anga?”
7 Yesu anayankha kuti: “Zimene ndikuchitazi sungazimvetse panopa, koma pambuyo pake udzamvetsa.”
8 Petulo anati: “Ndithu, sizitheka kuti musambitse mapazi anga.” Yesu anamuyankha kuti: “Ndikapanda kukusambitsa,+ palibe chako kwa ine.”
9 Simoni Petulo anati: “Ambuye, musandisambitse mapazi okha, koma mundisambitsenso manja ndi mutu womwe.”
10 Yesu anamuuza kuti: “Amene wasamba mʼthupi amangofunika kusamba mapazi okha basi, chifukwa thupi lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, koma osati nonsenu.”
11 Iye ankadziwa munthu amene anakonza zoti amupereke.+ Nʼchifukwa chake ananena kuti: “Sikuti nonsenu ndinu oyera.”
12 Tsopano atasambitsa mapazi awo nʼkuvalanso malaya ake akunja aja, anakhalanso patebulo. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa chifukwa chake ndasambitsa mapazi anu?
13 Inu mumanditchula kuti ‘Mphunzitsiʼ komanso ‘Ambuye,’ mumalondola, chifukwa ndinedi Mphunzitsi komanso Ambuye.+
14 Choncho ngati ine amene ndi Ambuye komanso Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu,+ inunso mukuyenera kusambitsana mapazi.+
15 Chifukwa ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.+
16 Ndithudi ndikukuuzani, kapolo saposa mbuye wake, ndiponso wotumidwa saposa amene wamutuma.
17 Ngati zimenezi mukuzidziwa, mudzakhala osangalala mukamazichita.+
18 Sindikunena nonsenu, ndikudziwa amene ndawasankha. Koma zimenezi zachitika kuti lemba likwaniritsidwe,+ limene limati: ‘Munthu amene ankadya chakudya changa, watukula chidendene chake nʼkundiukira.’*+
19 Kuyambira panopa kupita mʼtsogolo, ndizikuuziranitu zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire kuti amene munkamuyembekezera uja ndi ine.+
20 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense amene walandira yemwe ine ndamutuma walandiranso ine.+ Ndipo amene walandira ine, walandiranso amene anandituma.”+
21 Atanena zimenezi, Yesu anavutika kwambiri mumtima, ndipo anachitira umboni kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipereka.”+
22 Ophunzirawo anayamba kuyangʼanizana chifukwa sankadziwa kuti akunena ndani.+
23 Mmodzi wa ophunzirawo, amene Yesu ankamukonda,+ anakhala pafupi ndi Yesu.*
24 Choncho Simoni Petulo anamugwedezera mutu nʼkumuuza kuti: “Tiuze kuti akunena ndani.”
25 Ndiyeno wophunzira winayo anatsamira pachifuwa pa Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ambuye, mukunena ndani?”+
26 Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse mkate umene ndisunse.”+ Choncho atasunsa mkatewo, anapatsa Yudasi, mwana wa Simoni Isikariyoti.
27 Yudasi atalandira mkatewo, Satana analowa mwa iye.+ Choncho Yesu anamuuza kuti: “Zimene wakonza kuti uchite, zichite mwamsanga.”
28 Koma pa anthu amene anakhala nawo patebulowo, panalibe aliyense amene anadziwa chifukwa chake anamuuza zimenezo.
29 Popeza Yudasi ankasunga bokosi la ndalama,+ ena ankaganiza kuti Yesu ankamuuza kuti, “Ugule zinthu zonse zimene zikufunikira pachikondwerero,” kapena kuti apereke kenakake kwa osauka.
30 Choncho Yudasi atalandira mkatewo, anatuluka nthawi yomweyo ndipo unali usiku.+
31 Yudasi atatuluka, Yesu anati: “Tsopano Mwana wa munthu walemekezedwa,+ ndipo Mulungu walemekezedwa kudzera mwa iye.
32 Mulungu amulemekeza+ ndipo amulemekeza nthawi yomwe ino.
33 Anzanga apamtima inu,* ndikhala nanu kanthawi kochepa chabe. Mudzandifunafuna, ndipo mogwirizana ndi zimene ndinauza Ayuda aja kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kukafikako,’+ tsopano ndikuuzanso inuyo.
34 Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mofanana ndi mmene ine ndakukonderani,+ inunso muzikondana choncho.+
35 Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.”+
36 Simoni Petulo anamufunsa kuti: “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu anayankha kuti: “Kumene ndikupita sunganditsatire panopa, koma udzanditsatira mʼtsogolo.”+
37 Petulo anafunsanso kuti: “Ambuye, nʼchifukwa chiyani sindingakutsatireni panopa? Ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha inu.”+
38 Yesu anayankha kuti: “Kodi udzapereka moyo wako chifukwa cha ine? Ndithudi ndikukuuza iwe, tambala asanalire undikana katatu.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “wandiukira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anakhala pachifuwa pa Yesu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aangʼono inu.”