Wolembedwa ndi Yohane 15:1-27
15 “Ine ndine mtengo wa mpesa weniweni ndipo Atate wanga ndi mlimi.
2 Iwo amadula nthambi iliyonse mwa ine imene sikubereka zipatso ndipo iliyonse imene ikubereka zipatso amaiyeretsa poitengulira kuti ibereke zipatso zambiri.+
3 Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ine ndakuuzani.+
4 Mukhale ogwirizana ndi ine ndipo inenso ndikhala wogwirizana ndi inu. Mofanana ndi nthambi imene singabereke zipatso payokha, pokhapokha ngati ili yolumikizikabe kumpesawo, inunso simungabereke zipatso pokhapokha ngati muli olumikizika kwa ine.+
5 Ine ndine mtengo wa mpesa, inu ndinu nthambi zake. Aliyense amene ali wolumikizika kwa ine, inenso nʼkukhala wolumikizika kwa iye, amabereka zipatso zochuluka+ chifukwa simungathe kuchita chilichonse popanda ine.
6 Ngati munthu sapitiriza kukhala wolumikizika kwa ine, amaponyedwa kunja ngati nthambi ndipo amauma. Anthu amasonkhanitsa nthambi zoterozo nʼkuziponya pamoto ndipo zimapsa.
7 Mukapitiriza kukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.+
8 Atate amalemekezeka mukapitiriza kubereka zipatso zambiri komanso mukamasonyeza kuti ndinu ophunzira anga.+
9 Mofanana ndi Atate amene amandikonda,+ inenso ndimakukondani. Choncho pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse kuti ndizikukondanibe.
10 Mukamasunga malamulo anga mudzachititsa kuti nthawi zonse ndizikukondani, mofanana ndi ine amene ndimasunga malamulo a Atate nʼkuchititsa kuti nthawi zonse azindikonda.
11 Ndakuuzani zinthu zimenezi kuti mukhale ndi chimwemwe chimene ine ndili nacho komanso kuti chimwemwe chanu chisefukire.+
12 Ndikukulamulani kuti muzikondana mofanana ndi mmene ine ndimakukonderani.+
13 Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.+
14 Mukamachita zimene ndikukulamulani mukhala anzanga.+
15 Sindikukutchulaninso kuti akapolo chifukwa kapolo sadziwa zimene mbuye wake amachita. Koma ndakutchulani kuti anzanga, chifukwa ndakudziwitsani zinthu zonse zimene ndamva kwa Atate wanga.
16 Si inu amene munandisankha, koma ine ndinakusankhani kuti mupitirize kubereka zipatso zochuluka, komanso kuti zipatso zanuzo zisathe, kuti chilichonse chimene mungapemphe Atate mʼdzina langa akupatseni.+
17 Ndikukulamulani zinthu zimenezi nʼcholinga choti muzikondana.+
18 Ngati dziko likudana nanu, muzikumbukira kuti linayamba kudana ndi ine lisanadane ndi inu.+
19 Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake. Popeza simuli mbali ya dzikoli,+ koma ine ndinakusankhani kuchokera mʼdziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.+
20 Muzikumbukira mawu amene ndinakuuzani aja: Kapolo sangakhale wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.+ Ngati asunga mawu anga, adzasunganso mawu anu.
21 Koma adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha dzina langa, chifukwa amene anandituma ine sakumudziwa.+
22 Ndikanapanda kubwera kudzalankhula nawo, akanakhala opanda tchimo.+ Koma tsopano sangakane tchimo lawo.+
23 Aliyense amene amadana nane amadananso ndi Atate wanga.+
24 Ndikanapanda kuchita pamaso pawo ntchito zimene wina aliyense sanachitepo, akanakhala opanda tchimo.+ Koma tsopano andiona ndipo adana nane komanso adana ndi Atate wanga.
25 Zimenezi zachitika kuti mawu amene analembedwa mʼChilamulo akwaniritsidwe. Mawu ake ndi akuti: ‘Anadana nane popanda chifukwa.’+
26 Akadzafika mthandizi amene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, amene ndi mzimu wa choonadi+ wochokera kwa Atate, ameneyo adzandichitira umboni,+
27 ndipo inunso mudzandichitira umboni,+ chifukwa mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”