Yoswa 11:1-23
11 Yabini mfumu ya ku Hazori atangomva zimenezi, anatumiza uthenga woitanitsa Yobabi mfumu ya ku Madoni,+ mfumu ya ku Simironi ndi mfumu ya ku Akasafu.+
2 Anatumizanso uthenga kwa mafumu amʼdera lamapiri kumpoto, mafumu amʼchigwa* chakumʼmwera kwa Kinereti, mafumu a ku Sefela ndiponso mafumu okhala mʼmapiri a Dori+ kumadzulo.
3 Anaitanitsanso Akanani+ omwe ankakhala kumʼmawa ndi kumadzulo, ndiponso Aamori,+ Ahiti, Aperezi ndi Ayebusi akudera lamapiri. Komanso anaitanitsa Ahivi+ omwe ankakhala mʼmunsi mwa phiri la Herimoni+ ku Mizipa.
4 Choncho mafumuwo pamodzi ndi magulu awo onse ankhondo anabwera. Anali ambiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Ndipo anali ndi mahatchi* komanso magaleta* ankhondo ambirimbiri.
5 Mafumu onsewa anagwirizana kuti akumane pamodzi, ndipo anakamanga msasa pafupi ndi madzi a ku Meromu kuti amenyane ndi Aisiraeli.
6 Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino, ndidzawapereka onsewo kuti aphedwe ndi Aisiraeli. Mahatchi awo udzawapundule*+ ndipo magaleta awo udzawatenthe.”
7 Ndiyeno Yoswa ndi asilikali ake onse anafika modzidzimutsa pafupi ndi madzi a Meromu nʼkuyamba kupha adaniwo.
8 Yehova anapereka adaniwo mʼmanja mwa Aisiraeli.+ Choncho anayamba kuwagonjetsa ndipo anawathamangitsa mpaka kukafika kumzinda waukulu wa Sidoni,+ ku Misirepotu-maimu+ ndi kuchigwa cha Mizipe kumʼmawa. Anapitiriza kuwapha moti panalibe amene anapulumuka.+
9 Kenako Yoswa anachita zimene Yehova anamuuza. Mahatchi awo anawapundula ndipo magaleta awo anawatentha.+
10 Komanso Yoswa anabwerera nʼkukalanda mzinda wa Hazori ndipo anapha mfumu yake ndi lupanga,+ chifukwa poyamba mzinda wa Hazori unali likulu la maufumu onsewa.
11 Aisiraeliwo anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mumzindawo. Panalibe chamoyo chilichonse chimene chinatsala,+ ndipo Yoswa anatentha mzinda wa Hazori.
12 Yoswa analanda mizinda yonse ya mafumuwa, nʼkupha mafumu ake onse ndi lupanga+ mogwirizana ndi zimene Mose, mtumiki wa Yehova, analamula.
13 Komabe mizinda yonse imene inamangidwa pamalo okwera, Aisiraeli sanaitenthe. Mzinda wa Hazori wokha ndi umene Yoswa anautentha.
14 Aisiraeli anatenga katundu yense wa mʼmizindayi ndi ziweto zomwe.+ Koma anthu onse anawapha ndi lupanga.+ Sanasiye munthu aliyense wamoyo.+
15 Zimene Yehova analamula mtumiki wake Mose, Mose analamula Yoswa+ ndipo Yoswayo anachitadi zonse. Palibe chilichonse chimene Yoswa sanachite pa zonse zimene Yehova analamula Mose.+
16 Yoswa analanda dziko lonselo, dera lamapiri, dera lonse la Negebu,+ dziko lonse la Goseni, ku Sefela,+ ku Araba+ ndiponso dera lamapiri la Isiraeli ndi zigwa zake.
17 Analandanso dera lochokera kuphiri la Halaki lomwe lili moyangʼanizana ndi Seiri mpaka kukafika ku Baala-gadi,+ kuchigwa cha Lebanoni mʼmunsi mwa phiri la Herimoni.+ Yoswa anagonjetsa mafumu awo onse nʼkuwapha.
18 Iye anamenyana ndi mafumu onsewa kwa nthawi ndithu.
19 Panalibe mzinda winanso umene unagwirizana za mtendere ndi Aisiraeli, kupatulapo Ahivi a ku Gibiyoni.+ Aisiraeli anamenyana ndi mizinda ina yonse nʼkuigonjetsa.+
20 Yehova ndi amene analola kuti anthuwa aumitse mitima yawo+ kuti amenyane ndi Aisiraeli. Anatero kuti iye awawononge ndipo asawamvere chisoni,+ koma awatheretu mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.+
21 Pa nthawiyo Yoswa anapita nʼkukapha Aanaki+ onse kudera lamapiri, ku Heburoni, ku Debiri, ku Anabi, kudera lonse lamapiri la Yuda ndiponso kudera lonse lamapiri la Isiraeli. Yoswa anapha Aanaki onsewo nʼkuwononga mizinda yawo.+
22 Palibe Aanaki amene anatsala mʼdziko la Aisiraeli, kupatulapo+ amene ankakhala ku Gaza,+ ku Gati+ ndi ku Asidodi.+
23 Choncho Yoswa analanda dziko lonse mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza Mose.+ Kenako Yoswa anagawa dzikolo kwa Aisiraeli kuti likhale cholowa chawo, mogwirizana ndi mafuko awo.+ Ndipo mʼdziko lonselo munalibenso nkhondo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mafumu a ku Araba.”
^ Ena amati “mahosi.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Ankawapundula powadula mtsempha wakuseri kwa mwendo wakumbuyo.