Yoswa 18:1-28
18 Kenako gulu lonse la Aisiraeli linasonkhana ku Silo,+ ndipo kumeneko anamanga chihema chokumanako,+ popeza pa nthawiyo nʼkuti atagonjetsa dzikolo.+
2 Koma panali mafuko 7 a Aisiraeli amene anali asanagawiridwebe cholowa.
3 Choncho Yoswa anafunsa Aisiraeli kuti: “Kodi muzengereza mpaka liti osapita kukalanda dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani?+
4 Sankhani amuna atatu pa fuko lililonse oti ndiwatume. Akayendere dzikolo nʼkulemba mmene lilili kuti lidzagawidwe mogwirizana ndi cholowa cha mafuko awo. Akatero adzabwerere kwa ine.
5 Ndiyeno adzagawe dzikolo mʼzigawo 7.+ Fuko la Yuda lidzakhalabe kugawo lawo kumʼmwera,+ ndipo a mʼbanja la Yosefe adzakhalabe kugawo lawo kumpoto.+
6 Koma inuyo mukagawe dzikolo mʼzigawo 7 ndipo mukazilembe. Kenako mukabwere nazo kuno kuti ndidzakuchitireni maere+ pamaso pa Yehova Mulungu wathu.
7 Koma Alevi sadzapatsidwa gawo pakati panu,+ chifukwa cholowa chawo ndi unsembe wa Yehova.+ Fuko la Gadi, Rubeni ndi hafu ya fuko la Manase+ analandira kale cholowa chawo, chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa kutsidya lakumʼmawa la Yorodano.”
8 Choncho amuna aja anakonzeka kuti azipita, ndipo Yoswa anawalamula kuti: “Pitani mukayendere dzikolo nʼkulemba mmene lilili. Mukatero mukabwere kuno, ndipo ndidzakuchitirani maere pamaso pa Yehova ku Silo kuno.”+
9 Amunawo anapitadi kukayendera dzikolo ndipo analigawa mʼzigawo 7 potsatira mizinda yake nʼkulemba mʼbuku. Atamaliza anabwerera kwa Yoswa kumsasa ku Silo.
10 Kenako Yoswa anawachitira maere pamaso pa Yehova ku Silo+ ndipo anagawira Aisiraeli dzikolo moti fuko lililonse analipatsa gawo limodzi.+
11 Maere oyamba anagwera fuko la Benjamini motsatira mabanja awo, ndipo anapatsidwa dera limene linali pakati pa ana a Yuda+ ndi ana a Yosefe.+
12 Kumpoto, malire a gawo lawo anayambira ku Yorodano nʼkupitirira kukafika kumalo otsetsereka akumpoto kwa Yeriko,+ nʼkukwera phiri chakumadzulo, nʼkukathera kuchipululu cha Beti-aveni.+
13 Malirewo anapitirira kukafika kumʼmwera kwa malo otsetsereka otchedwa Luzi, kutanthauza Beteli.+ Kuchokera ku Luzi anatsetserekera ku Ataroti-adara,+ nʼkukadutsa paphiri lakumʼmwera kwa Beti-horoni Wakumunsi.+
14 Kumadzulo kwa gawolo, malirewo anakhotera kumʼmwera, paphiri loyangʼanizana ndi kumʼmwera kwa Beti-horoni. Kuchokera pamenepo anakathera ku Kiriyati-baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu,+ womwe ndi mzinda wa Yuda. Amenewa ndi malire akumadzulo a gawo la Benjamini.
15 Malire akumʼmwera a gawolo anayambira kumapeto kwa Kiriyati-yearimu, nʼkulowera chakumadzulo, nʼkupitirira kukafika kukasupe wa madzi a Nafitoa.+
16 Malirewo anakafika kumapeto kwa phiri loyangʼanizana ndi chigwa cha Mwana wa Hinomu,+ limene linathera kumpoto kwa chigwa cha Arefai.+ Kenako anatsetserekera kuchigwa cha Hinomu kumʼmwera kwa malo otsetsereka otchedwa Yebusi+ mpaka kukafika ku Eni-rogeli.+
17 Analowera chakumpoto nʼkukafika ku Eni-semesi mpaka kumzinda wa Gelilotu, womwe uli kutsogolo kwa chitunda cha Adumi.+ Kuchokera pamenepo, anatsetserekera kumwala+ wa Bohani,+ mwana wa Rubeni.
18 Anapitirira nʼkukafika kumalo otsetsereka akumpoto amene ali kutsogolo kwa Araba, nʼkutsetsereka kukafika ku Araba.
19 Malirewo anapitirira mpaka kumalo otsetsereka akumpoto kwa Beti-hogila,+ nʼkukathera kugombe lakumpoto kwa Nyanja Yamchere,*+ kumapeto kwa mtsinje wa Yorodano mbali yakumʼmwera. Awa anali malire akumʼmwera a gawo la Benjamini.
20 Kumʼmawa, malire ake anali mtsinje wa Yorodano. Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini motsatira mabanja awo, ndi malire ake kuzungulira gawo lonse.
21 Mizinda ya fuko la Benjamini motsatira mabanja awo inali Yeriko, Beti-hogila, Emeki-kezizi,
22 Beti-araba,+ Zemaraimu, Beteli,+
23 Aavi, Para, Ofira,
24 Kefara-amoni, Ofini ndi Geba.+ Mizinda 12 ndi midzi yake.
25 Kunalinso Gibiyoni,+ Rama, Beeroti,
26 Mizipe, Kefira, Moza,
27 Rekemu, Iripeeli, Tarala,
28 Zela,+ Ha-elefi, Yebusi, kutanthauza Yerusalemu,+ Gibea+ ndi Kiriyati. Mizinda 14 ndi midzi yake.
Chimenechi chinali cholowa cha ana a Benjamini motsatira mabanja awo.
Mawu a M'munsi
^ Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.