Yoswa 22:1-34

  • Mafuko akumʼmawa anabwerera kwawo (1-8)

  • Anamanga guwa ku Yorodano (9-12)

  • Anafotokoza cholinga cha guwa (13-29)

  • Anagwirizananso (30-34)

22  Kenako Yoswa anaitana anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase, 2  nʼkuwauza kuti: “Mwachita zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani,+ ndiponso mwamvera zonse zimene ine ndinakulamulani.+ 3  Simunawasiye abale anu nthawi yonseyi mpaka lero+ ndipo mwasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu.+ 4  Panopa Yehova Mulungu wanu wapatsa abale anu mpumulo mogwirizana ndi zimene anawalonjeza.+ Choncho bwererani, mupite kumatenti anu kudera limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani, kutsidya lina* la Yorodano.+ 5  Koma mukaonetsetse kuti mukutsatira Chilamulo ndiponso malamulo amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani.+ Muzikakonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda mʼnjira zake zonse,+ kumvera malamulo ake,+ kumʼmamatira+ ndiponso kumʼtumikira+ ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse.”+ 6  Kenako Yoswa anawadalitsa nʼkuwauza kuti azipita ndipo anapita kumatenti awo. 7  Mose anali atapatsa hafu ya fuko la Manase cholowa chawo ku Basana.+ Hafu ina ya fukolo, Yoswa anaipatsa cholowa pamodzi ndi abale awo kutsidya lina la Yorodano kumadzulo.+ Komanso pamene Yoswa ankawauza kuti azipita kumatenti awo, anawadalitsa. 8  Anawauza kuti: “Bwererani kumatenti anu ndi chuma chambiri, ziweto zambiri, siliva, golide, kopa, zitsulo ndi zovala zambiri.+ Tengani katundu amene munakatenga+ kwa adani anu ndipo mukagawane ndi abale anu.” 9  Zitatero, anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase, anachoka ku Silo kumene kunali Aisiraeli mʼdziko la Kanani. Anabwerera ku Giliyadi,+ kudera limene Mose anawapatsa molamulidwa ndi Yehova kuti azikhalako.+ 10  Atafika kuchigawo cha Yorodano chimene chinali mʼdziko la Kanani, anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase anamanga guwa lansembe mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano, ndipo guwalo linali lalikulu komanso logometsa. 11  Kenako Aisiraeli ena anamva+ anthu akunena kuti: “Eti anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase amanga guwa lansembe mʼmalire a dziko la Kanani, mʼchigawo cha Yorodano kumbali ya Aisiraeli.” 12  Aisiraeli atamva zimenezi, gulu lawo lonse linasonkhana ku Silo+ kuti apite kukamenyana nawo. 13  Kenako Aisiraeli anatumiza Pinihasi+ mwana wa wansembe Eleazara, kwa anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase, ku Giliyadi. 14  Anamʼtumiza pamodzi ndi atsogoleri 10. Fuko lililonse la Isiraeli linatumiza mtsogoleri mmodzi woimira nyumba ya makolo ake. Mtsogoleri aliyense anali woimira nyumba ya bambo ake pakati pa Aisiraeli masauzande.+ 15  Atafika kwa anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase ku Giliyadi, anawauza kuti: 16  “Anthu onse a Yehova anena kuti: ‘Nʼchifukwa chiyani mwachita zosakhulupirika+ kwa Mulungu wa Isiraeli? Lero mwasiya kutsatira Yehova pomanga guwa lanu lansembe kuti mupandukire Yehova.+ 17  Kodi zoipa zimene tinachita ku Peori zatichepera? Sitinadziyeretsebe ku tchimo limene lija mpaka lero, ngakhale kuti mliri unagwera anthu a Yehova.+ 18  Kodi inuyo tsopano mukufuna kusiya kutsatira Yehova? Mukapandukira Yehova lero, ndiye kuti mawa adzakwiyira gulu lonse la Aisiraeli.+ 19  Ngati chili chifukwa choti dziko lanu ndi lodetsedwa, wolokerani kudziko la Yehova+ kumene kuli tenti yopatulika ya Yehova*+ ndipo muzikakhala nafe. Koma musapandukire Yehova, ndipo musachititse ifeyo kupanduka chifukwa cha guwa lansembe limene mwamangali, kuwonjezera pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu.+ 20  Akani+ mwana wa Zera atachita zosakhulupirika potenga zinthu zoyenera kuwonongedwa, kodi mkwiyo sunagwere gulu lonse la Aisiraeli?+ Ndipo iye sanafe yekha chifukwa cha cholakwa chakecho.’”+ 21  Atamva zimenezi, anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase anayankha atsogoleri a masauzande a Aisiraeliwo, kuti:+ 22  “Yehova, Mulungu wa milungu! Yehova, Mulungu wa milungu!+ Iye akudziwa ndipo nawonso Aisiraeli adziwa. Ngati tachita zimenezi chifukwa chopanduka ndiponso chifukwa choti ndife osakhulupirika kwa Yehova, musatisiye amoyo lero. 23  Ngati tadzimangira guwa lansembe kuti tisiye kutsatira Yehova ndiponso ngati timafuna kuti tiziperekerapo nsembe zopsereza ndi nsembe zambewu komanso nsembe zachiyanjano, Yehova apereka yekha chilango.+ 24  Koma ife tinamanga guwa lansembeli chifukwa choda nkhawa kuti, ‘Mʼtsogolo muno ana anu adzauza ana athu kuti: “Mulibe ufulu woti muzilambira Yehova Mulungu wa Isiraeli. 25  Yehova anaika malire pakati pa ife ndi inuyo a fuko la Rubeni ndi la Gadi. Malire ake ndi mtsinje wa Yorodano. Inuyo zolambira Yehova sizikukukhudzani.” Ndipo ana anu adzalepheretsa ana athu kulambira* Yehova.’ 26  Nʼchifukwa chake tinati: ‘Tiyeni timange guwa, osati loperekerapo nsembe zopsereza kapena nsembe zina, 27  koma kuti ukhale umboni pakati pa ife ndi inu+ komanso ana athu,* wakuti tidzatumikira Yehova ndi nsembe zathu zopsereza, nsembe zachiyanjano ndi nsembe zina,+ kuti mʼtsogolo ana anu asadzauze ana athu kuti: “Inuyo zolambira Yehova sizikukukhudzani.”’ 28  Choncho tinati, ‘Akadzatiuza zimenezi ifeyo kapena ana athu mʼtsogolo, tidzawauza kuti: “Onani guwa lansembe limene makolo athu anamanga lofanana ndi guwa la Yehova, osati kuti aziperekerapo nsembe zopsereza kapena nsembe zina, koma kuti likhale umboni pakati pa inu ndi ife.”’ 29  Nʼzosatheka kuti ife lero tipandukire Yehova, nʼkusiya kutsatira Yehova+ pomanga guwa lansembe loti tiziperekerapo nsembe zopsereza, zambewu ndi nsembe zina, kusiya guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, limene lili patsogolo pa tenti yake yopatulika!”+ 30  Wansembe Pinihasi, atsogoleri a gulu la Aisiraeli ndiponso atsogoleri a masauzande a Aisiraeli amene anali naye, atamva mawu amene ana a Rubeni, a Gadi ndi a Manase ananena, anakhutira.+ 31  Ndiyeno Pinihasi mwana wa wansembe Eliezara, anauza ana a Rubeni, a Gadi ndi a Manase, kuti: “Lero tadziwa kuti Yehova ali pakati pathu chifukwa simunachite zosakhulupirika kwa Yehova. Apatu mwapulumutsa Aisiraeli mʼdzanja la Yehova.” 32  Kenako Pinihasi mwana wa wansembe Eliezara ndi atsogoleri aja, anachoka kwa anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ku Giliyadi, nʼkubwerera kwa Aisiraeli ena ku Kanani. Ndipo anawafotokozera zimene anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ananena. 33  Aisiraeliwo atamva zimenezi anakhutira ndipo anatamanda Mulungu. Sananenenso zopita kukamenyana ndi fuko la Rubeni ndi la Gadi kapena kukawononga dera limene ankakhala. 34  Choncho anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi analitcha dzina guwalo,* chifukwa anati, “Guwali ndi mboni pakati pathu kuti Yehova ndi Mulungu woona.”

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi mbali yakumʼmawa.
Kapena kuti, “chihema chopatulika cha Yehova.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuopa.”
Kapena kuti, “komanso mibadwo yobwera pambuyo pathu.”
Guwalo ayenera kuti analitcha dzina lakuti, “Mboni.”