Yoswa 23:1-16
23 Tsopano Yoswa anali atakalamba ndiponso anali ndi zaka zambiri.+ Apa nʼkuti patapita masiku ambiri kuchokera pamene Yehova anapatsa Aisiraeli mpumulo+ powapulumutsa kwa adani awo onse owazungulira.
2 Yoswa anaitana Aisiraeli onse,+ akulu awo, atsogoleri, oweruza ndi akapitawo+ nʼkuwauza kuti: “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri.
3 Inuyo mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu anachitira mitundu yonseyi chifukwa cha inu. Yehova Mulungu wanu ndi amene ankakumenyerani nkhondo.+
4 Ndinakupatsani malo a mitundu yonse imene yatsalayi pochita maere.+ Ndinakupatsaninso malo a mitundu imene ndinaiwononga+ kuchokera kumtsinje wa Yorodano mpaka ku Nyanja Yaikulu* chakumadzulo,* kuti akhale cholowa cha mafuko anu.+
5 Yehova Mulungu wanu ndi amene ankawachotsa pamaso panu,+ ndipo anawathamangitsa chifukwa cha inu. Inu munatenga malo awo mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulonjezani.+
6 Tsopano limbani mtima kwambiri kuti muzitsatira zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la Chilamulo+ cha Mose, ndipo musapite kudzanja lamanja kapena lamanzere.+
7 Ndiponso muzipewa kugwirizana* ndi mitundu+ imene yatsala pakati panu. Musamatchule nʼkomwe mayina a milungu yawo+ kapena kulumbira pa milunguyo, ndipo musamaitumikire kapena kuigwadira.+
8 Koma muyenera kumamatira Yehova Mulungu wanu+ ngati mmene mwakhala mukuchitira mpaka lero.
9 Yehova adzathamangitsa mitundu ikuluikulu ndiponso yamphamvu kuichotsa kwa inu+ chifukwa mpaka pano, palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene wakwanitsa kulimbana nanu.+
10 Munthu mmodzi yekha wa inu adzathamangitsa anthu 1,000,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu akukumenyerani nkhondo+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani.+
11 Choncho muzikonda Yehova Mulungu wanu+ ndipo mukamachita zimenezi, mudzateteza miyoyo yanu nthawi zonse.+
12 Koma mukasiya Mulungu nʼkumamatira anthu a mitundu ina, amene atsala pakati panuwa+ nʼkumakwatirana nawo+ komanso kumagwirizana nawo,
13 dziwani kuti Yehova Mulungu wanu adzasiya kuwathamangitsa pamaso panu.+ Iwo adzakhala ngati msampha ndiponso ngati khwekhwe kwa inu. Adzakhalanso ngati zikwapu kumsana kwanu+ komanso ngati zitsotso mʼmaso mwanu, mpaka mutatheratu mʼdziko labwino limene Yehova Mulungu wanu wakupatsanili.
14 Tsopano ine ndatsala pangʼono kufa. Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti palibe mawu ngakhale amodzi pa malonjezo onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena, omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.+
15 Koma mofanana ndi malonjezo onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena omwe akwaniritsidwa pa inu,+ Yehova adzakwaniritsanso pa inu masoka onse* amene ananena, ndipo adzakufafanizani padziko labwino limene Yehova Mulungu wanu wakupatsanili.+
16 Mukadzaphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu limene anakulamulani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira, Yehova adzakukwiyirani kwambiri+ ndipo simudzachedwa kutha padziko labwino limene iye anakupatsani.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “kolowera dzuwa.”
^ Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.
^ Kapena kuti, “muzipewa kusakanikirana.”
^ Kapena kuti, “mawu oipa onse.”