Yoswa 4:1-24

  • Miyala ya chikumbutso (1-24)

4  Mtundu wonse utangomaliza kuwoloka mtsinje wa Yorodano, Yehova anauza Yoswa kuti: 2  “Tenga amuna 12 pakati pa anthuwa, mwamuna mmodzi pa fuko lililonse.+ 3  Uwalamule kuti, ‘Pitani pakati pa mtsinje wa Yorodano, pamene ansembe aima+ ndipo mukatengepo miyala 12 nʼkupita nayo kumene mukagone usiku wa lero.’”+ 4  Choncho Yoswa anaitana amuna 12 amene anawasankha pakati pa Aisiraeli, mwamuna mmodzi pa fuko lililonse. 5  Ndipo anawauza kuti: “Dutsani kutsogolo kwa Likasa la Yehova Mulungu wanu, mukafike pakati pa mtsinje wa Yorodano. Aliyense akanyamule mwala umodzi paphewa pake, mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Aisiraeli. 6  Miyalayo idzakhala chizindikiro kwa inu. Ana anu* akamadzafunsa mʼtsogolo muno kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 7  Muzidzawauza kuti: ‘Nʼchifukwa chakuti madzi amumtsinje wa Yorodano anagawikana chifukwa cha likasa+ la pangano la Yehova. Likasalo likudutsa mumtsinje wa Yorodano, madzi a mtsinjewo anagawikana. Miyalayi ndi yoti izikumbutsa Aisiraeli zimenezo mpaka kalekale.’”+ 8  Choncho Aisiraeliwo anachita zimene Yoswa anawalamula. Anapita pakati pa mtsinje wa Yorodano, ndipo anakanyamula miyala 12 mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Aisiraeli, ngati mmene Yehova analamulira Yoswa. Ananyamula miyalayo nʼkupita nayo kumalo amene anagona. 9  Komanso Yoswa anatenga miyala 12 nʼkuisanja pakati pa mtsinje wa Yorodano, pamalo amene ansembe onyamula likasa la pangano anaima.+ Miyalayo ilipo mpaka lero. 10  Ansembe onyamula Likasawo, anaimabe pakati pa mtsinje wa Yorodano, mpaka zonse zimene Yehova analamula Yoswa kuti auze anthuwo zitachitika, mogwirizana ndi zonse zimene Mose analamula Yoswa. Ansembewo ali chiimire choncho, anthuwo anawoloka mtsinjewo mofulumira. 11  Anthu onse atangotha kuwoloka, Likasa la Yehova linawoloka litanyamulidwa ndi ansembewo, anthu onsewo akuona.+ 12  Anthu a fuko la Rubeni, a fuko la Gadi komanso hafu ya fuko la Manase, anawoloka nʼkumayenda patsogolo pa Aisiraeli ena atakonzekera kumenya nkhondo,+ ngati mmene Mose anawalangizira.+ 13  Amuna pafupifupi 40,000 onyamula zida anawoloka nʼkupita kuchipululu cha Yeriko, ndipo Yehova anali nawo. 14  Pa tsikuli, Yehova anachititsa Aisiraeli onse kuona kuti Yoswa ndi mtsogoleri wamkulu,+ ndipo anayamba kumulemekeza* kwambiri masiku onse a moyo wake ngati mmene ankalemekezera Mose.+ 15  Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: 16  “Lamula ansembe onyamula likasa+ la Umboni kuti achoke mumtsinje wa Yorodano.” 17  Choncho Yoswa analamula ansembewo kuti: “Tulukani mumtsinje wa Yorodano.” 18  Ansembe onyamula likasa+ la pangano la Yehova atachoka pakati pa mtsinje wa Yorodano, komanso mapazi awo atangoponda pamtunda, madzi a mtsinjewo anayambanso kuyenda ndipo anasefukira mbali zonse+ ngati poyamba. 19  Anthuwo anawoloka mtsinje wa Yorodano pa tsiku la 10 la mwezi woyamba ndipo anakamanga msasa ku Giligala,+ kumalire a kumʼmawa kwa Yeriko. 20  Miyala 12 imene anaitenga mumtsinje wa Yorodano ija, Yoswa anaisanja ku Giligala.+ 21  Kenako anauza Aisiraeli kuti: “Mʼtsogolomu ana anu akamadzafunsa abambo awo kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 22  Muzidzauza anawo kuti, ‘Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano panthaka youma.+ 23  Izi zinachitika pamene Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano, mpaka iwo atawoloka. Zinachitika mofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anachita pa Nyanja Yofiira, pamene anaphwetsa madzi a nyanjayo, mpaka onse atawoloka.+ 24  Yehova anachita zimenezi kuti anthu onse apadziko lapansi adziwe kuti dzanja lake ndi lamphamvu,+ ndiponso kuti inu muziopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse.’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana anu aamuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumuopa.”