Yoweli 2:1-32
2 “Lizani lipenga mu Ziyoni.+
Lengezani mʼphiri langa loyera kuti kukubwera nkhondo.
Anthu onse okhala mʼdzikoli anjenjemere,Chifukwa tsiku la Yehova likubwera+ ndipo lili pafupi.
2 Limeneli ndi tsiku lamdima ndi lachisoni,+Tsiku lamitambo ndi lamdima wandiweyani.+Tsikuli lili ngati mmene kuwala kwa mʼbandakucha kumaonekera pamwamba pa mapiri.
Pali mtundu wa anthu ambiri ndiponso amphamvu.+Kuyambira kalekale, palibenso mtundu wina womwe ungafanane nawo,Ndipo sikudzakhalanso mtundu wina wofanana nawo,Kumibadwomibadwo.
3 Kutsogolo kwawo moto ukuwononga,Ndipo kumbuyo kwawo malawi amoto akusakaza.+
Dziko lomwe lili patsogolo pawo lili ngati munda wa Edeni,+Koma kumbuyo kwawo kuli chipululu,Ndipo palibe chilichonse chingapulumuke.
4 Mtundu wa anthuwo umaoneka ngati mahatchi,*Ndipo amathamanga ngati mahatchi ankhondo.+
5 Amadumphadumpha ndipo amachita mkokomo ngati magaleta oyenda pamwamba pa mapiri,+Ndiponso ngati moto walawilawi umene ukutentha mapesi.
Ali ngati anthu amphamvu omwe ayalana pokonzekera kumenya nkhondo.+
6 Anthu adzakhala ndi nkhawa chifukwa cha mtunduwo.
Nkhope zawo zonse zidzakhala zamantha.
7 Amathamanga ngati asilikali.Amakwera khoma ngati asilikali.Aliyense amayenda mʼnjira yake,Ndipo saphonya njira zawo.
8 Iwo sakankhanakankhana.Aliyense amayenda mʼnjira yake.
Wina akalasidwa nʼkugwa,Enawo sabwerera mʼmbuyo.
9 Iwo amathamangira mʼmizinda ndipo amathamanga pakhoma la mpanda.
Amakwera nyumba ndipo amalowera pawindo ngati mbala.
10 Dzombelo likamayenda, dziko limanjenjemera ndipo kumwamba kumagwedezeka.
Dzuwa ndi mwezi zada,+Ndipo nyenyezi zasiya kuwala.
11 Yehova adzawalankhula asilikali ake mokweza+ chifukwa anthu amumsasa wake ndi ambiri.+
Amene akukwaniritsa mawu ake ndi wamphamvu.Tsiku la Yehova ndi lalikulu komanso lochititsa mantha.+
Ndani angalimbe pa tsiku limeneli?”+
12 Yehova wanenanso kuti, “Tsopano bwererani kwa ine ndi mtima wonse.+Salani kudya,+ lirani momvetsa chisoni ndiponso mokweza.
13 Ngʼambani mitima yanu,+ osati zovala zanu,+Ndipo bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,Chifukwa iye ndi wachifundo, wokoma mtima, wosakwiya msanga+ ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.+Iye adzasintha maganizo okubweretserani tsoka.
14 Ndani akudziwa kuti mwina adzasintha maganizo,+Ndipo adzakusiyirani madalitso,Nsembe yambewu ndi nsembe yachakumwa kuti mupereke kwa Yehova Mulungu wanu?
15 Lizani lipenga mu Ziyoni.
Lengezani za nthawi yosala kudya. Itanitsani msonkhano wapadera.+
16 Sonkhanitsani anthu ndipo muyeretse mpingo.+
Sonkhanitsani amuna achikulire,* ana komanso makanda.+
Mkwati atuluke mʼchipinda chake ndipo nayenso mkwatibwi atuluke mʼchipinda chake.
17 Pakati pa khonde ndi guwa la nsembe,+Ansembe omwe ndi atumiki a Yehova alire nʼkumanena kuti:
‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu,Ndipo musachititse manyazi cholowa chanu,Kuti anthu a mitundu ina awalamulire.
Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+
18 Ndiyeno Yehova adzachitira nsanje dziko lake,Ndipo adzachitira chifundo anthu ake.+
19 Yehova adzayankha anthu ake kuti:
‘Ndikukutumizirani mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta.Anthu inu mudzakhuta.+Sindidzachititsanso kuti muzinyozedwa pakati pa anthu a mitundu ina.+
20 Mdani wakumpoto ndidzamuthamangitsira kutali ndi inu.Ndidzamuthamangitsira kudziko louma komanso lopanda anthu,Nkhope yake itayangʼana kunyanja yakumʼmawa,*Nkhongo yake italoza kunyanja yakumadzulo.*
Fungo lake lonunkha lidzamveka,Ndipo fungo lake loipalo lidzafalikira mʼdziko lonselo,+Chifukwa Mulungu adzachita zinthu zazikulu.’
21 Usachite mantha iwe dziko.
Sangalala chifukwa Yehova adzachita zinthu zazikulu.
22 Inu zilombo zakutchire musachite mantha,Chifukwa malo odyetserako ziweto kutchire adzamera msipu wobiriwira.+Mitengo nayonso idzabereka zipatso.+Mtengo wa mkuyu ndi mtengo wa mpesa udzabereka zipatso zambiri.+
23 Inu ana aamuna a Ziyoni sangalalani chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera,Ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi,Mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+
24 Malo opunthira mbewu adzadzaza ndi mbewu,Ndipo malo opangira vinyo komanso mafuta adzasefukira.+
25 Ndidzakubwezerani mbewu za zaka zonseZimene dzombe, ana a dzombe opanda mapiko komanso dzombe losakaza zinadya.Limeneli ndi gulu langa lankhondo limene ndinakutumizirani.+
26 Mudzadya nʼkukhuta,+Ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,+Amene wakuchitirani zodabwitsa.Anthu anga sadzachitanso manyazi mpaka kalekale.+
27 Mudzadziwa kuti ine ndili pakati pa Isiraeli,+Komanso kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu+ ndipo palibenso wina.
Anthu anga sadzachitanso manyazi mpaka kalekale.
28 Zimenezi zikadzachitika ndidzapereka* mzimu wanga+ kwa chamoyo chilichonse,Ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosera.Amuna achikulire adzalota maloto,Ndipo anyamata adzaona masomphenya.+
29 Ngakhale akapolo anga aamuna ndi aakazi,Ndidzawapatsa mzimu wanga mʼmasiku amenewo.
30 Ndidzachita zodabwitsa kumwamba ndi padziko lapansi.Padzakhala magazi, moto ndi utsi wambiri wokwera mʼmwamba.+
31 Dzuwa lidzasanduka mdima ndipo mwezi udzasanduka magazi,+Tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova lisanafike.+
32 Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka,+Chifukwa mʼphiri la Ziyoni ndiponso mu Yerusalemu mudzakhala anthu opulumuka+ ngati mmene Yehova ananenera.Anthu opulumuka amene Yehova akuwaitana.”
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “mahosi.”
^ Kapena kuti, “akulu.”
^ Kutanthauza “Nyanja Yakufa.”
^ Kutanthauza “Nyanja ya Mediterranean.”
^ Kapena kuti, “ndidzatsanulira.”