Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Zekariya

Machaputala

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14

Mitu

  • 1

    • Kuuza anthu kuti abwerere kwa Yehova (1-6)

      • ‘Bwererani kwa ine ndipo ine ndidzabwerera kwa inu’ (3)

    • Masomphenya Oyamba: Okwera pamahatchi ataima pamitengo ya mchisu (7-17)

      • “Yehova adzalimbikitsanso Ziyoni” (17)

    • Masomphenya Achiwiri: Nyanga 4 ndi amisiri 4 (18-21)

  • 2

    • Masomphenya Achitatu: Munthu atanyamula chingwe choyezera (1-13)

      • Kuyeza Yerusalemu (2)

      • Yehova, “mpanda wamoto” (5)

      • Kukhudza mwana wa diso la Mulungu (8)

      • Mitundu yambiri ya anthu idzakhala kumbali ya Yehova (11)

  • 3

    • Masomphenya a 4: Kusintha zovala za mkulu wa ansembe (1-10)

      • Satana ankatsutsa Mkulu wa Ansembe Yoswa (1)

      • “Ndibweretsa mtumiki wanga dzina lake Mphukira” (8)

  • 4

    • Masomphenya a 5: Choikapo nyale ndi mitengo iwiri ya maolivi (1-14)

      • ‘Sipakufunika mphamvu, koma mzimu wanga’ (6)

      • Asakunyozeni chifukwa munayamba ndi zinthu zochepa (10)

  • 5

    • Masomphenya a 6: Mpukutu ukuuluka (1-4)

    • Masomphenya a 7: Chiwiya chokwana muyezo wa efa (5-11)

      • Munali mzimayi dzina lake Kuipa (8)

      • Chiwiya anachitenga nʼkupita nacho ku Sinara (9-11)

  • 6

    • Masomphenya a 8: Magaleta 4 (1-8)

    • Mphukira idzakhala mfumu ndi wansembe (9-15)

  • 7

    • Yehova anadzudzula anthu osala kudya mwachinyengo (1-14)

      • “Kodi munkasaladi kudya chifukwa cha ine?” (5)

      • ‘Muzisonyeza chilungamo, chikondi chokhulupirika ndi chifundo’ (9)

  • 8

    • Yehova anapatsa Ziyoni mtendere ndi choonadi (1-23)

      • Yerusalemu, “mzinda wa choonadi” (3)

      • “Muziuzana zoona” (16)

      • Kusiya kusala kudya nʼkuyamba kuchita chikondwerero (18, 19)

      • ‘Tifunefune Yehova’ (21)

      • Amuna 10 adzagwira mkanjo wa Myuda (23)

  • 9

    • Mulungu adzaweruza anthu a mitundu ina (1-8)

    • Kubwera kwa mfumu ya Ziyoni (9, 10)

      • Mfumu yodzichepetsa inakwera bulu (9)

    • Anthu a Yehova adzamasulidwa (11-17)

  • 10

    • Pemphani mvula kwa Yehova osati kwa milungu yabodza (1, 2)

    • Yehova akugwirizanitsa anthu ake (3-12)

      • Mtsogoleri wochokera mʼbanja la Yuda (3, 4)

  • 11

    • Zotsatira za kukana mʼbusa weniweni wa Mulungu (1-17)

      • “Weta nkhosa zimene zinayenera kuphedwa” (4)

      • Ndodo ziwiri: Wosangalatsa komanso Mgwirizano (7)

      • Malipiro a mʼbusa: Ndalama 30 zasiliva (12)

      • Ndalama zinaponyedwa mosungira chuma (13)

  • 12

    • Yehova anateteza Yuda ndi Yerusalemu (1-9)

      • Yerusalemu, “mwala wolemera” (3)

    • Kulirira munthu amene anabayidwa (10-14)

  • 13

    • Kuchotsa mafano ndi aneneri abodza (1-6)

      • Aneneri abodza adzachita manyazi (4-6)

    • Mʼbusa adzaphedwa (7-9)

      • Anthu otsala adzayengedwa (9)

  • 14

    • Kulambira koona kudzapambana (1-21)

      • Phiri la Maolivi lidzagawikana pakati (4)

      • Yehova adzakhala mmodzi, dzina lake lidzakhala limodzi (9)

      • Mliri wa anthu otsutsa Yerusalemu (12-15)

      • Chikondwerero cha Misasa (16-19)

      • Mphika uliwonse udzakhala woyera kwa Yehova (20, 21)