Zekariya 8:1-23
8 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba analankhula nanenso kuti:
2 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: ‘Ndatsimikiza mtima kuti ndidzateteza Ziyoni.+ Ndatsimikiza kuti ndidzamuteteza nditakwiya kwambiri.’”
3 “Yehova wanena kuti, ‘Ndidzabwerera ku Ziyoni+ ndipo ndizidzakhala ku Yerusalemu.+ Yerusalemu adzatchedwa mzinda wa choonadi*+ ndipo phiri la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba lidzatchedwa phiri loyera.’”+
4 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Amuna ndi akazi achikulire adzakhalanso mʼmabwalo a mzinda wa Yerusalemu, aliyense atanyamula ndodo mʼmanja mwake chifukwa cha ukalamba.*+
5 Mʼmabwalo a mzindawo mudzadzaza anyamata ndi atsikana ndipo azidzasewera mmenemo.’”+
6 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ngakhale kuti pa nthawiyo anthu omwe adzatsale adzaona kuti zimenezo nʼzosatheka, kodi zidzakhalanso zosatheka kwa ine?’ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”
7 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ine ndipulumutsa anthu anga kuchokera kudziko lakumʼmawa ndiponso lakumadzulo.+
8 Ndidzawabweretsa, ndipo azidzakhala mu Yerusalemu.+ Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo+ woona* ndi wachilungamo.’”
9 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Limbani mtima ndipo mukonzeke kugwira ntchito,+ inu amene mukumva mawu a aneneri+ masiku ano. Awa ndi mawu amene ananenedwanso tsiku limene maziko a nyumba ya Yehova wa magulu ankhondo akumwamba anayalidwa kuti kachisi amangidwe.
10 Nthawi imeneyi isanafike, palibe malipiro omwe ankaperekedwa polipira munthu kapena chiweto.+ Zinali zoopsa kuyenda ulendo chifukwa cha adani, popeza ine ndinkachititsa kuti anthu onse aziukirana.’
11 ‘Koma tsopano anthu anga otsala sindidzawachitiranso zinthu ngati mmene ndinachitira masiku akale,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
12 ‘Mʼdzikolo mudzadzalidwa mbewu ya mtendere. Mpesa udzabala zipatso ndipo dziko lapansi lidzatulutsa zokolola zake.+ Kumwamba kudzagwetsa mame ndipo ndidzachititsa kuti anthu otsala alandire zinthu zonsezi.+
13 Popeza munali temberero pakati pa anthu a mitundu ina,+ inu a mʼnyumba ya Yuda ndi a mʼnyumba ya Isiraeli ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala dalitso.+ Limbani mtima,+ musachite mantha.’+
14 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘“Monga zinalili kuti ndinatsimikiza mtima kukugwetserani tsoka chifukwa choti makolo anu anandikwiyitsa ndipo sindinakumvereni chisoni,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,
15 “panopa ndatsimikizanso mtima kuchitira zabwino Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda.+ Choncho musachite mantha.”’+
16 ‘Muzichita zinthu izi: Muziuzana zoona.+ Poweruza milandu mʼmageti a mizinda yanu, muziweruza mogwirizana ndi choonadi komanso molimbikitsa mtendere.+
17 Musamakonzerane chiwembu mumtima mwanu+ ndipo musamakonde kulumbira monama.+ Chifukwa zinthu zonsezi ndimadana nazo,’+ watero Yehova.”
18 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba analankhula nanenso kuti:
19 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Kusala kudya kwa mʼmwezi wa 4,+ kusala kudya kwa mʼmwezi wa 5,+ kusala kudya kwa mʼmwezi wa 7+ ndiponso kusala kudya kwa mʼmwezi wa 10,+ idzakhala nthawi yachikondwerero komanso yosangalala kwa anthu a mʼnyumba ya Yuda.+ Choncho muzikonda choonadi ndiponso mtendere.’
20 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ndithu anthu a mitundu ina ndi anthu amʼmizinda yambiri adzabwera.
21 Ndipo anthu amumzinda wina adzapita kwa anthu amumzinda wina nʼkuwauza kuti: “Tiyeni tipite tikapemphe Yehova kuti atikomere mtima* komanso tikafunefune Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Inenso ndipita nawo.”+
22 Anthu ambiri a mitundu ina ndiponso mitundu yamphamvu idzabwera kudzafunafuna Yehova wa magulu ankhondo akumwamba mu Yerusalemu,+ ndiponso kudzapempha Yehova kuti awakomere mtima.’*
23 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Mʼmasiku amenewo, amuna 10 ochokera mʼzilankhulo zonse za anthu a mitundu ina+ adzagwira mkanjo* wa Myuda nʼkunena kuti: “Anthu inu tikufuna tipite nanu limodzi,+ chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”’”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “wokhulupirika.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa cha kuchuluka kwa masiku.”
^ Kapena kuti, “wokhulupirika.”
^ Kapena kuti, “timukhazike mtima pansi.”
^ Kapena kuti, “timukhazike mtima pansi.”
^ Kapena kuti, “mʼmunsi mwa chovala.”