Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 10

Kodi Baibulo Limalonjeza Chiyani Zamʼtsogolo?

“Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.”

Salimo 37:29

“Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”

Mlaliki 1:4

“Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”

Yesaya 25:8

“Pa nthawi imeneyo, maso a anthu amene ali ndi vuto losaona adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu amene ali ndi vuto losamva adzayamba kumva. Pa nthawi imeneyo, munthu wolumala adzadumpha ngati mmene imachitira mbawala, ndipo lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mosangalala. Mʼchipululu mudzatumphuka madzi, ndipo mʼdera lachipululu mudzayenda mitsinje.”

Yesaya 35:​5, 6

“Iye adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka. Zakalezo zapita.”

Chivumbulutso 21:4

“Iwo adzamanga nyumba nʼkumakhalamo, ndipo adzadzala minda ya mpesa nʼkudya zipatso zake. Sadzamanga nyumba kuti wina azikhalamo, kapena kudzala kuti ena adye. Chifukwa masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo, ndipo anthu anga osankhidwa adzasangalala mokwanira ndi ntchito ya manja awo.”

Yesaya 65:21, 22