Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 A2

Zimene Zili MʼBaibuloli

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba a Chigiriki Achikhristu linatulutsidwa mʼChingelezi mu 1950, ndipo Baibulo la Dziko Latsopano lonse lathunthu linatulutsidwa mu 1961. Kuchokera nthawi imeneyo, anthu mamiliyoni ambiri omwe amalankhula zilankhulo zoposa 210 akhala akuwerenga Malemba Opatulikawa, omwe anamasuliridwa molondola kuchokera ku zilankhulo zoyambirira ndipo ndi osavuta kuwerenga.

Komabe, kwa zaka zoposa 50 zapitazo, zilankhulo zakhala zikusintha. Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano imene ilipo panopa inazindikira kuti ikufunika kuchitapo kanthu nʼcholinga choti anthu akamawerenga Baibulo masiku ano, liziwafika pamtima. Chifukwa cha zimenezi, mʼBaibuloli akonzanso zina ndi zina kuti likhale lomveka bwino kwambiri. Pochita zimenezi anaganizira mfundo zotsatirazi:

  • Kugwiritsa ntchito mawu osavuta kumva amene anthu akumagwiritsa ntchito masiku ano. Mwachitsanzo, mawu a Chingelezi amene poyamba ankawagwiritsa ntchito pomasulira mawu akuti “kuleza mtima,” ankachititsa anthu kuganiza za “munthu amene wavutika kwa nthawi yaitali.” Koma tanthauzo lolondola ndi kuchita zinthu modekha, limene limafotokozedwa bwino ndi mawu akuti “kuleza mtima.” (Agalatiya 5:22) MʼBaibulo la Chingelezi munali mawu ena amene kale ankatanthauza “munthu wosalankhula” koma panopa tanthauzoli linasintha. Choncho mawuwo anachotsedwa ndipo mʼmalomwake anaikamo ena amene anthu akugwiritsa ntchito masiku ano. (Mateyu 9:32, 33) Mawu akuti “mkazi wadama” anasinthidwa kukhala “hule.” (Genesis 38:15) MʼBaibuloli, mawu kuti “dama” mʼmalo ambiri anawamasulira kuti “chiwerewere.” Mawu akuti “khalidwe lotayirira” anawamasulira kuti “khalidwe lopanda manyazi,” ndipo mawu akuti “maphwando aphokoso” anawamasulira kuti “maphwando oipa.” (Agalatiya 5:19-21) Mawu akuti “kunthawi zosatha” anasinthidwa ndipo mʼmalomwake anagwiritsa ntchito mawu akuti “mpaka kalekale,” “mpaka muyaya,” “kwamuyaya” kapena “akale,” mogwirizana ndi tanthauzo la chiganizo chilichonse.—Genesis 3:22; Salimo 48:14; Salimo 146:10; Mlaliki 1:4; Mika 5:2.

    MʼChiheberi komanso mʼChigiriki chakale, mawu akuti “mbewu” ankatanthauza mbewu za zomera komanso ana a anthu, mbadwa kapena umuna. Popeza anthu masiku ano sakugwiritsanso ntchito mawu akuti “mbewu” ponena za anthu, mawuwa anasinthidwa ndipo mʼmalomwake anagwiritsa ntchito mawu amene akupereka tanthauzo loyenera mogwirizana ndi chiganizo chilichonse. (Genesis 1:11; 22:17; 48:4; Mateyu 22:24; Yohane 8:37) Panopa mʼmalo ambiri agwiritsa ntchito mawu akuti “mbadwa” ponena za lonjezo la mu Edeni lomwe lili pa Genesis 3:15.

  • Kufotokoza mawu ena a mʼBaibulo. Baibuloli likufotokoza kuti Yesu anafera pamtengo wozunzikirapo, osati pamtanda. Pa Mateyu 10:38, Maliko 8:34 ndi mʼmalemba ena, anagwiritsa ntchito mawu akuti “mtengo wozunzikirapo” komanso anaikapo mawu amʼmunsi amene akulozera owerenga ku Matanthauzo a Mawu Ena. Ku Matanthauzo a Mawu Enako kuli tanthauzo la mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “mtengo wozunzikirapo.” Komanso pa Mateyu 5:22, 29, 30, Maliko 9:43 ndi pa Luka 12:5 anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti “Gehena” mʼmalo mwa mawu akuti “helo.” Mʼmavesi amenewa muli mawu amʼmunsi amene akulozera owerenga ku Matanthauzo a Mawu Ena kumene kuli tanthauzo la mawu akuti “Gehena.” Mʼmalo ambiri, mawu a Chiheberi akuti cheʹsedh anamasuliridwa kuti “chikondi chokhulupirika” chifukwa limeneli ndi tanthauzo limene olemba Baibulo mʼchilankhulo cha Chihebericho ankafuna.—Ekisodo 34:6; Rute 3:10.

    Kulemba ziganizo zosavuta kuwerenga. Pofuna kuonetsetsa kuti ziganizo nʼzosavuta kuwerenga komanso ndi zomveka bwino, anayesetsa kupewa mawu ovuta komanso ziganizo zitalizitali. MʼBaibuloli, analemba mawu ngati mmene anthu amalankhulira. Mwachitsanzo, onani Genesis 3:9-13, Rute 1:8-13 ndi Aheberi 12:1. Akafuna kusintha chilichonse mʼBaibuloli, ankachita zinthu mosamala kwambiri, ankaipempherera nkhaniyo komanso ankalemekeza kwambiri ntchito yaikulu imene abale a mʼkomiti yoyambirira yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano anagwira.

Zinthu zina zimene zili mʼBaibuloli:

MʼBaibuloli muli mawu amʼmunsi osiyanasiyana. Mawu amʼmunsiwa anagawidwa mʼmagulu otsatirawa:

  • “Kapena kuti” Mawu amʼmunsi amenewa amapereka njira zina zomasulirira mawu a Chiheberi, Chiaramu kapena Chigiriki zomwe zikupereka tanthauzo lomwelo.—Genesis 1:2, mawu amʼmunsi pa mawu akuti “Mphamvu ya Mulungu inkayendayenda”; Yoswa 1:8, “kuganizira mozama.”

  • “Mabaibulo ena amati” Mawu amʼmunsi amenewa amapereka njira zina zovomerezeka zomasulirira mawuwo koma zimene zikupereka tanthauzo losiyana.—Genesis 21:6, “asangalala nane limodzi”; Zekariya 14:21, “munthu wa ku Kanani.”

  • “Mʼchilankhulo choyambirira” Mawu amʼmunsi amenewa amamasulira liwu ndi liwu mawu a Chiheberi, Chiaramu kapena Chigiriki. Kapenanso amapereka tanthauzo la mawu a chilankhulo choyambirira.—Genesis 30:22, “ayambe kubereka”; Genesis 3:15, “mbadwa.”

  • Tanthauzo komanso mfundo zina zothandiza Mawu amʼmunsi amenewa amapereka matanthauzo a mayina (Genesis 3:17, “Adamu”; Ekisodo 15:23, “Mara”); mfundo zokhudza kulemera kwa zinthu komanso miyezo yake (Genesis 6:15, “mamita 134”); mlowamʼmalo wa dzina (Salimo 55:20, “Iye”); kusonyeza mfundo zothandiza zimene zili ku Zakumapeto komanso ku Matanthauzo a Mawu Ena.—Genesis 37:35, “Manda”; Mateyu 5:22, “Gehena.”

Koyambirira kwa Baibuloli kuli gawo lakuti, “Kodi MʼBaibulo Muli Nkhani Zotani?” Mʼgawo limeneli muli mfundo zoyambirira za mʼBaibulo zimene munthu akuyenera kuziphunzira. Mukangomaliza buku la Chivumbulutso, mupeza mitu yakuti “Mayina a Mabuku a MʼBaibulo,” “Kalozera wa Mawu a MʼBaibulo” komanso “Matanthauzo a Mawu Ena.” Matanthauzo a Mawu Ena amathandiza owerenga kuti amvetse mawu ena mogwirizana ndi mmene awagwiritsira ntchito mʼBaibulo. Mu Zakumapeto A, muli nkhani zotsatirazi: “Mfundo Zimene Anatsatira Pomasulira Baibulo,” “ Zimene Zili MʼBaibuloli,” “Zimene Zinachitika Kuti Baibulo Lisungike Mpaka Pano,” “Dzina la Mulungu MʼMalemba a Chiheberi,” “Dzina la Mulungu MʼMalemba a Chigiriki,” “Tchati: Aneneri Komanso Mafumu a Yuda ndi Isiraeli” komanso “Zinthu Zikuluzikulu Zimene Yesu Anachita Ali Padziko Lapansi.” Mu Zakumapeto B muli mapu, matchati ndi mfundo zina zothandiza kwa anthu amene akufuna kuphunzira Baibulo mozama.

Buku lililonse la mʼBaibulo lili ndi gawo limene likufotokoza mwachidule zimene zili mʼchaputala chilichonse komanso mavesi ake. Zimenezi zimathandiza owerenga kukhala ndi chithunzi cha nkhani zimene zili mʼbuku lonselo. Danga limene lili pakati pa tsamba lililonse lili ndi malifalensi omwe achokera mʼBaibulo lathu lakale ndipo akusonyeza mavesi ena amene ali ndi mfundo zofanana.