Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Nkhani Zatsopano Zothandiza Poyamba Kukambirana ndi Anthu

Nkhani Zatsopano Zothandiza Poyamba Kukambirana ndi Anthu

Kuyambira January 2016, tsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda yogawira likumakhala ndi nkhani yakuti “Kodi Baibulo Limanena Zotani?” Cholinga cha nkhani zimenezi n’kutithandiza kuyamba kukambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Nkhanizi zikumalembedwa mofanana ndi timapepala. Zikumakhala ndi funso lothandiza munthu kufotokoza maganizo ake, yankho la m’Malemba la funsolo komanso mfundo zowonjezera zomwe tingathe kukambirana ndi munthu.

Nthawi zambiri, anthu omwe takambirana nawo bwino mfundo za m’Malemba amayamba kuphunzira Baibulo. Tikukulimbikitsani kuti muzigwiritsa ntchito nkhani zatsopanozi kuti muthandize anthu ambiri omwe akufunafuna choonadi.—Mat. 5:6.

MMENE TINGAGWIRITSIRE NTCHITO NKHANIZI:

  1. Pemphani munthu amene mukumulalikira kuti afotokoze maganizo ake pa funso limodzi

  2. Mvetserani yankho lake ndipo muyamikireni

  3. Werengani lemba lomwe lili pakamutu kakuti “Zimene Baibulo Limanena.” Ndiyeno m’pempheni kuti afotokoze maganizo ake palembalo. Ngati ali ndi nthawi, mungakambirane naye mfundo zomwe zili pakamutu kakuti, “Mfundo Zinanso Zomwe Tikuphunzira M’Baibulo.”

  4. Perekani magaziniyo

  5. Konzani zoti mudzakumanenso ndi kukambirana funso lachiwiri