MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo za Ufumu Zimatithandiza Kukhala Olimba Mtima
Paulo ndi Sila ali m’ndende ankatamanda Mulungu poimba nyimbo. (Mac. 16:25) Nawonso Akhristu anzathu omwe anali kundende ya Sachsenhausen, pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi ku Germany komanso ena omwe anali mu ukapolo ku Siberia, ankaimba nyimbo za Ufumu. Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti nyimbo zimalimbikitsa kwambiri Akhristu pa nthawi ya mavuto.
Posachedwapa buku la nyimbo la mutu wakuti Imbirani Yehova Mosangalala, liyamba kupezeka m’zinenero zambiri. Choncho tikangopeza bukuli, tiyesetse kuloweza mawu a nyimbozi. Tingamayeserere kuimba pa nthawi ya kulambira kwa pabanja. (Aef. 5:19) Tikamachita zimenezi, mzimu woyera udzatithandiza kukumbukira nyimbozi pa nthawi imene tili m’mavuto. Nyimbo za Ufumu zimatithandizanso kuti tiziganizira kwambiri za zinthu zimene tikuyembekezera. Choncho zingatilimbikitse tikakumana ndi mavuto. Komanso pa nthawi imene zinthu zili bwino tingathe ‘kuimba mosangalala’ chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima. (1 Mbiri 15:16; Sal. 33:1-3) Ndiye tiyeni tiyesetse kuti tizizidziwa bwino nyimbo zathu za Ufumu.
ONERANI VIDIYO YAKUTI NYIMBO IMENE INALIMBIKITSA AKAIDI. KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachititsa kuti M’bale Frost alembe nyimbo?
-
Kodi nyimboyi inalimbikitsa bwanji abale omwe anali ku ndende ya Sachsenhausen?
-
Kodi nyimbo za Ufumu zingatilimbikitse bwanji pa zochita zathu zatsiku ndi tsiku?
-
Kodi ndi nyimbo za Ufumu ziti zimene mukufuna kuti muziloweze?