Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

April 16-22

MALIKO 1-2

April 16-22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • Machimo Ako Akhululukidwa”: (10 min.)

    • [Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Maliko.]

    • Maliko 2:3-5​—Mwachifundo, Yesu anakhululukira machimo a munthu wakufa ziwalo (jy 67 ¶3-5)

    • Maliko 2:6-12​—Pamene anachiritsa munthu wakufa ziwalo, Yesu anasonyeza kuti ali ndi mphamvu yokhululukira machimo (“Chapafupi n’chiti” mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 2:9, nwtsty)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

    • Maliko 1:11​—Kodi Yehova ankatanthauza chiyani pamene analankhula mawu amenewa kwa Yesu? (“panamveka mawu ochokera kumwamba” “Iwe ndiwe Mwana wanga” “ndimakondwera nawe” mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 1:11, nwtsty)

    • Maliko 2:27, 28​—N’chifukwa chiyani Yesu anadzitchula kuti ndi “Mbuye wa Sabata”? (“Mbuye wa sabata” mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 2:28, nwtsty)

    • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

    • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Maliko 1:1-15

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Yambani ndi chitsanzo cha zimene tinganene. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri.

  • Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene.

  • Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 44

  • “Sindinabwere Kudzaitana Anthu Olungama, Koma Ochimwa”: (7 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo yakuti Zinthu Zinayamba Kuyenda Bwino. Kenako funsani mafunso otsatirawa: N’chiyani chimene chinathandiza Donald kuti ayambe kukhala wosangalala? Tikamalalikira, kodi tingatengere bwanji Yesu pochita zinthu mopanda tsankho?​—Maliko 2:17.

  • Yehova Amakhululuka “ndi Mtima Wonse”: (8 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Yehova, Ndikufuna Mukhale Pamalo Oyamba. Kenako funsani mafunso otsatirawa: Kodi n’chifukwa chiyani Anneliese anabwerera kwa Yehova ndipo zinatheka bwanji? (Yes. 55:6, 7) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji zimene zinamuchitikirazi pothandiza ena omwe anasiya kutumikira Yehova?

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 16¶18-24 komanso tsamba 178 ndi 181

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

  • Nyimbo Na. 86 ndi Pemphero