MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tizigwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa
Kupanga ophunzira kuli ngati kumanga nyumba. Kuti munthu amange nyumba amafunika kuphunzira mmene angagwiritsire ntchito mwaluso zida zake zomangira. Nafenso tiyenera kuphunzira kugwiritsa ntchito mwaluso chida chathu chachikulu chomwe ndi Baibulo. (2 Tim. 2:15) Tiyeneranso kumagwiritsa ntchito bwino mabuku ndi mavidiyo omwe timagwiritsa ntchito pophunzitsa n’cholinga choti tipange ophunzira. *
Kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa? (1) Pemphani woyang’anira kagulu kanu kuti akuthandizeni, (2) muzilalikira limodzi ndi ofalitsa aluso kapena apainiya, komanso (3) muziyeserera nthawi zonse. Mukamagwiritsa ntchito mabuku komanso mavidiyo athu mwaluso, muzisangalala kwambiri kugwira ntchito yomanga mwauzimu yomwe ikuchitika masiku ano.
MAGAZINI
TIMABUKU
MABUKU
TIMAPEPALA
MAVIDIYO
TIMAPEPALA TOITANIRA
MAKADI
^ ndime 3 Pali mabuku ena omwe sali m’gulu la Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa, omwe analembedwera anthu ena. Mukhoza kugwiritsa ntchito mabuku amenewa ngati pakufunika kutero.