MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kulalikira Komanso Kuphunzitsa N’kofunika Kwambiri Kuti Tipange Ophunzira
Yesu analamula otsatira ake kuti athandize anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake. (Mat. 28:19) Kuti zimenezi zitheke pamafunika kulalikira komanso kuphunzitsa. Nthawi zonse tiyenera kumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndizilalikira komanso kuphunzitsa anthu mwaluso muutumiki?’
KULALIKIRA
M’malo modikira kuti anthu abwere kwa ife, tiyenera kupita n’kumakafufuza anthu amene ‘ali oyenerera.’ (Mat. 10:11) Tikakhala mu utumiki, kodi timakhala tcheru kuti tilankhule ndi aliyense amene takumana naye? (Mac. 17:17) Lidiya anakhala wophunzira chifukwa chakuti Paulo ankalalikira mwakhama.—Mac. 16:13-15.
ONERANI VIDIYO YAKUTI, PITIRIZANI KULALIKIRA “MWAKHAMA”—MWAMWAYI KOMANSO KUNYUMBA NDI NYUMBA KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRIWA:
-
Kodi Samuel anasonyeza bwanji kuti tsiku lililonse ankafunitsitsa kubzala mbewu za choonadi?
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizigwiritsa ntchito njira zonse zolalikirira?
-
Kodi tingamalalikire kwa ndani pamene tikuchita zinthu zatsiku ndi tsiku?
KUPHUNZITSA
Kuti tipange ophunzira, si zokwanira kumangosiyira magazini anthu omwe timawapeza. Tiyenera kumapanga maulendo obwereza ndiponso kumachititsa maphunziro a Baibulo n’cholinga chofuna kuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. (1 Akor. 3:6-9) Koma bwanji ngati anthu amene tikuchita khama kuti tiwaphunzitse za Ufumu wa Mulungu alibe chidwi? (Mat. 13:19-22) Tiyenera kufufuzabe anthu amene mitima yawo ili ngati ‘nthaka yabwino.’—Mat. 13:23; Mac. 13:48.
ONERANI VIDIYO YAKUTI, PITIRIZANI KULALIKIRA “MWAKHAMA”—M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI KOMANSO MUZITHANDIZA ANTHU KUTI AKHALE OPHUNZIRA A YESU KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi a Solomon ndi akazi awo anatani kuti athirire mbewu za choonadi mumtima mwa a Ezekiel ndi akazi awo?
-
Kodi cholinga chathu chizikhala chotani tikamagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira kuphatikizapo kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri?
-
Kodi tingatani kuti tizilimbikira kugwira ntchito yophunzitsa ena choonadi?