April 8-14
1 AKORINTO 10-13
Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova ndi Wokhulupirika”: (10 min.)
1 Akor. 10:13—Yehova samachita kusankha mayesero oti tingakumane nawo (w17.02 29-30)
1 Akor. 10:13—Mayesero amene timakumana nawo ndi amenenso “amagwera anthu ena”
1 Akor. 10:13—Yehova angatithandize kupirira mayesero alionse tikamamudalira
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
1 Akor. 10:8—N’chifukwa chiyani vesili limanena kuti Aisiraeli amene anaphedwa tsiku limodzi chifukwa chochita dama analipo 23,000 pomwe pa Numeri 25:9 pamati analipo 24,000? (w04 4/1 29)
1 Akor. 11:5, 6, 10—Kodi mlongo ayenera kuvala chinachake kumutu akamachititsa phunziro ali ndi m’bale amene ndi wofalitsa? (w15 2/15 30)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) 1 Akor. 10:1-17 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 1)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri. (th phunziro 3)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Musonyezeni chimodzi mwa Zinthu Zophunzitsira. (th phunziro 6)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
‘Ziwalo Zonse za Thupi ndi Zofunika’ (1 Akor. 12:22): (10 min.) Onerani vidiyoyi.
“Kodi Muchikonzekera Bwanji Chikumbutso?”: (5 min.) Nkhani. Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito nyengo ya Chikumbutsoyi kuganizira za kufunika kwa mwambowu ndiponso chikondi chimene Yehova komanso Yesu anatisonyeza.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 33
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 116 ndi Pemphero