Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Muchikonzekera Bwanji Chikumbutso?

Kodi Muchikonzekera Bwanji Chikumbutso?

Kuyambira chaka chino, tizikhala ndi nthawi yambiri yokonzekera Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Chikumbutso chikakhala m’kati mwa mlungu, sitizikhala ndi msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu. Komanso ngati chingakhale kumapeto kwa mlungu, sitizikhala ndi nkhani ya onse komanso Phunziro la Nsanja ya Olonda. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji nthawi imeneyi? Mofanana ndi zomwe zinkachitika m’nthawi ya atumwi, pali zambiri zimene tingachite pokonzekera mwambowu. (Luka 22:7-13; km 3/15 1) Komabe, tiyeneranso kukonzekeretsa mtima wathu. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

Ofalitsa ena amawerenga Baibulo komanso kuganizira mavesi a pa nyengo ya Chikumbutso opezeka m’kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku. Ena amawerenga mavesi a m’Baibulo omwe ali patchati chili m’munsichi. Komanso ena amawerenganso nkhani za mu Nsanja ya Olonda zokhudza Chikumbutso komanso zofotokoza chikondi chimene Yehova ndi Yesu anatisonyeza. Njira iliyonse imene mungasankhe ingakuthandizeni kuyandikira kwambiri Yehova ndi Mwana wake.