Yehova ndi Wokhulupirika
Ngakhale kuti Yehova akhoza kutichotsera mayesero, nthawi zambiri amapereka “njira yopulumukira.” Iye amachita zimenezi potipatsa zinthu zofunikira kuti tithe kupirira mayesero omwe takumana nawo.
-
Angatithandize kuti maganizo ndi mtima wathu zikhale m’malo pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake woyera komanso zinthu zauzimu zomwe amatipatsa.—Mat. 24:45; Yoh. 14:16; Aroma 15:4
-
Akhoza kutitsogolera pogwiritsa ntchito mzimu woyera womwe ungatithandize kukumbukira mfundo komanso zitsanzo za anthu a m’Baibulo. Angatithandizenso kuganizira njira yabwino yomwe tingasankhe.—Yoh. 14:26
-
Akhozanso kugwiritsa ntchito angelo ake kuti atithandize.—Aheb. 1:14
-
Angagwiritsenso ntchito abale ndi alongo athu.—Akol. 4:11