Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

April 6-12

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu Udzachitika Lachiwiri pa 7 April, 2020

April 6-12

Chaka chilichonse panyengo ya Chikumbutso, Akhristu ambiri amaganizira chikondi chachikulu chimene Yehova ndi Mwana wake Yesu Khristu anatisonyeza. (Yoh 3:16; 15:13) Gwiritsani ntchito tchati chili m’munsichi kuti mupeze malemba omwe akufotokoza zimene zinachitika m’nthawi yomaliza ya utumiki wa Yesu ku Yerusalemu. Zomwe zinachitikazo zinafotokozedwa m’chigawo 6 cha buku la Yesu​—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo. Kodi chikondi chomwe Mulungu komanso Khristu anakusonyezani chimakulimbikitsani bwanji?​—2Ak 5:14, 15; 1Yo 4:16, 19.

MASIKU OMALIZA A UTUMIKI WA YESU KU YERUSALEMU

Nthawi

Malo

Zimene Zinachitika

Mateyu

Maliko

Luka

Yohane

33 C.E., Nisani 8 (1-2 April, 2020)

Betaniya

Yesu anafika ku Betaniya kutatsala masiku 6 kuti Pasika achitike

 

 

 

11:55–12:1

Nisani 9 (2-3 April, 2020)

Betaniya

Mariya anathira Yesu mafuta m’mutu ndi m’mapazi

26:6-13

14:3-9

 

12:2-11

Betaniya-Betefage-Yerusalemu

Analowa mu Yerusalemu mwaulemerero, atakwera bulu

21:1-11, 14-17

11:1-11

19:29-44

12:12-19

Nisani 10 (3-4 April, 2020)

Betaniya-Yerusalemu

Anatemberera mtengo wa mkuyu; kenako anayeretsanso kachisi

21:18, 19; 21:12, 13

11:12-17

19:45, 46

 

Yerusalemu

Ansembe aakulu ndi alembi anakonza chiwembu choti aphe Yesu

 

11:18, 19

19:47, 48

 

Mawu a Yehova anamveka; Yesu ananeneratu za imfa yake; Ayuda sanamukhulupirire ndipo zimenezi zinakwaniritsa ulosi wa Yesaya

 

 

 

12:20-50

Nisani 11 (4-5 April, 2020)

Betaniya-Yerusalemu

Anaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito mtengo wa mkuyu womwe unafota

21:19-22

11:20-25

 

 

Yerusalemu, kachisi

Anthu anakaikira ulamuliro wa Khristu; fanizo la ana awiri aamuna

21:23-32

11:27-33

20:1-8

 

Mafanizo: alimi omwe anapha anthu, phwando la ukwati

21:33–22:14

12:1-12

20:9-19

 

Yesu anayankha mafunso okhudza Mulungu komanso Kaisara, kuuka kwa akufa, lamulo lalikulu kwambiri

22:15-40

12:13-34

20:20-40

 

Yesu anafunsa anthu ngati Khristu ali mwana wa Davide

22:41-46

12:35-37

20:41-44

 

Anadzudzula mwamphamvu alembi ndi Afarisi

23:1-39

12:38-40

20:45-47

 

Anaona mkazi wamasiye akupereka ndalama

 

12:41-44

21:1-4

 

Phiri la Maolivi

Ananena za chizindikiro cha kukhalapo kwake

24:1-51

13:1-37

21:5-38

 

Mafanizo: anamwali 10, matalente, nkhosa ndi mbuzi

25:1-46

 

 

 

Nisani 12 (5-6 April, 2020)

Yerusalemu

Atsogoleri achiyuda anakonza zoti amuphe

26:1-5

14:1, 2

22:1, 2

 

Yudasi anakonza zomupereka

26:14-16

14:10, 11

22:3-6

 

Nisani 13 (6-7 April, 2020)

Pafupi ndi Yerusalemu komanso mkati mwake

Anakonzekera Pasika womaliza

26:17-19

14:12-16

22:7-13

 

Nisani 14 (7-8 April, 2020)

Yerusalemu

Anadya Pasika ndi atumwi ake

26:20, 21

14:17, 18

22:14-18

 

Anasambitsa mapazi a atumwi ake

 

 

 

13:1-20

Yesu ananena kuti Yudasi ndi yemwe adzamupereke ndipo anamuuza kuti achoke

26:21-25

14:18-21

22:21-23

13:21-30

Anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye (1Ak 11:23-25)

26:26-29

14:22-25

22:19, 20, 24-30

 

Ananeneratu kuti Petulo adzamukana komanso kuti atumwi adzabalalika

26:31-35

14:27-31

22:31-38

13:31-38

Analonjeza kuti adzatumiza mthandizi; fanizo la mpesa; anapereka lamulo la chikondi; anapemphera komaliza ndi atumwi ake

 

 

 

14:1–17:26

Getsemane

Anavutika maganizo; anaperekedwa ndi kumangidwa

26:30, 36-56

14:26, 32-52

22:39-53

18:1-12

Yerusalemu

Anafunsidwa mafunso ndi Anasi; anazengedwa mlandu ndi Kayafa, Khoti Lalikulu la Ayuda; Petulo anamukana

26:57–27:1

14:53–15:1

22:54-71

18:13-27

Yudasi amene anapereka Yesu anadzimangirira (Mac 1:18, 19)

27:3-10

 

 

 

Anaonekera kwa Pilato, Herode, kenako anabwereranso kwa Pilato

27:2, 11-14

15:1-5

23:1-12

18:28-38

Pilato anayesetsa kuti amumasule koma Ayuda anasankha kuti awamasulire Baraba; anaweruzidwa kuti aphedwe mochita kupachikidwa pamtengo

27:15-30

15:6-19

23:13-25

18:39–19:16

(cha m’ma 3 koloko madzulo)

Gologota

Anafa atamupachika pamtengo

27:31-56

15:20-41

23:26-49

19:16-30

Yerusalemu

Anatsitsa thupi lake pamtengo n’kukaliika m’manda

27:57-61

15:42-47

23:50-56

19:31-42

Nisani 15 (8-9 April, 2020)

Yerusalemu

Ansembe ndi Afarisi anatseka pamandapo n’kuikapo alonda

27:62-66

 

 

 

Nisani 16 (9-10 April, 2020)

Yerusalemu ndi madera apafupi; Emau

Yesu anaukitsidwa; anaonekera maulendo 5 kwa ophunzira ake

28:1-15

16:1-8

24:1-49

20:1-25

Pambuyo pa Nisani 16

Yerusalemu; Galileya

Anaonekeranso maulendo angapo kwa ophunzira ake (1Ak 15:5-7; Mac 1:3-8); anawalangiza; ndi kuwalamula kuti agwire ntchito yophunzitsa anthu

28:16-20

 

 

20:26–21:25