April 13-19
GENESIS 31
Nyimbo Na. 112 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yakobo ndi Labani Anachita Pangano Lamtendere”: (10 min.)
Ge 31:44-46—Yakobo ndi Labani anaunjika mulu wamiyala pomwe anadyerapo chakudya choimira pangano (it-1 883 ¶1)
Ge 31:47-50—Anatchula malowa kuti Galeeda ndiponso Nsanja ya Mlonda (it-2 1172)
Ge 31:51-53—Analonjezana kuti mabanja awo adzakhala mwamtendere
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Ge 31:19—N’chifukwa chiyani Rakele anaba aterafi a bambo ake? (it-2 1087-1088)
Ge 31:41, 42—Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yakobo ngati timagwira ntchito kwa mabwana “ovuta kuwakondweretsa”? (1Pe 2:18; w13 3/15 21 ¶8)
Kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Ge 31:1-18 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi mlongoyu anathandiza bwanji munthuyo kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundo ya lemba limene anawerenga? Kodi anachita zotani kuti adzapange ulendo wobwereza?
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 4)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 5 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako mugawireni kabuku ka Uthenga Wabwino n’kuyamba kuphunzira naye phunziro 5. (th phunziro 8)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzilimbikitsa Amene Afooka : (Osapitirira 20 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Onerani vidiyo yakuti Yehova Amasamalira Nkhosa Zake. Kenako fotokozani mwachikondi mfundo zingapo zapatsamba 14 m’kabuku kakuti Bwererani kwa Yehova.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 80
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (Osapitirira 3 min.)
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero