Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Chofunika Kwambiri kwa Ine N’chiyani?

Kodi Chofunika Kwambiri kwa Ine N’chiyani?

Yakobo analimbana ndi mngelo kuti apeze chinthu chofunika kwambiri chomwe ndi madalitso ochokera kwa Yehova. (Ge 32:24-31; Ho 12:3, 4) Nanga bwanji ifeyo? Kodi timayesetsa kumvera Yehova kuti atidalitse? Mwachitsanzo, ngati zitachitika kuti patsiku la misonkhano tikufunika kugwira ovataimu, kodi tingasankhe kuchita chiyani? Tikamayesetsa kutumikira Yehova pomupatsa nthawi yathu, mphamvu zathu komanso chuma chathu, iye adzatikhuthulira ‘madalitso oti tidzasowa powalandirira.’ (Mki 3:10) Komanso adzatitsogolera, kutiteteza ndiponso kutipatsa zofunikira pamoyo wathu.​—Mt 6:33; Ahe 13:5.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUSASIYE KUKHALA NDI ZOLINGA ZAUZIMU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi mlongoyu anayesedwa bwanji ndi zinthu zimene ankazikonda?

  • Kodi ntchito yathu ingakhale bwanji chiyeso?

  • N’chifukwa chiyani Timoteyo ankafunika kupitirizabe kukhala ndi zolinga ngakhale anali wolimba mwauzimu?​—1Ti 4:16

  • Kodi chinthu chofunika kwambiri pamoyo wanu n’chiyani?

    Kodi zochita zathu zingasonyeze bwanji kuti timaona kuti kutumikira Yehova ndikofunika kwambiri pamoyo wathu?