Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 32-33

Kodi Mukuyesetsa Kuchita Zonse Zomwe Mungathe Kuti Mupeze Madalitso?

Kodi Mukuyesetsa Kuchita Zonse Zomwe Mungathe Kuti Mupeze Madalitso?

32:24-28

Kuti Yehova atidalitse, tiyenera kuchita khama kwambiri komanso kuonetsetsa kuti kutumikira Yehova kuzikhala pamalo oyamba pamoyo wathu. (1Ak 9:26, 27) Ngakhale kuti Yakobo anali wachikulire, anasonyeza khama ndipo nafenso tiyenera kutengera chitsanzo chake. Tingasonyeze kuti timafunitsitsa kuti Yehova atidalitse . . .

  • Tikamakonzekera bwino misonkhano yampingo

  • Tikamalalikira nthawi zonse

  • Tikamayesetsa kuthandiza ena mumpingo

Kaya tikukumana ndi mavuto otani, tiyenera kumapemphera kwa Yehova nthawi zonse kuti atithandize komanso kumamutumikira ndi mtima wonse kuti atidalitse.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndi zinthu ziti zomwe ndikufunika kuyesetsa kumazichita mwakhama kuti Yehova azindidalitsa?’