Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Chotsani Milungu Yachilendo”

“Chotsani Milungu Yachilendo”

Yakobo ankadziwa kuti ayenera kulambira Yehova yekha ngakhale kuti pa nthawiyo Mulungu anali asanapereke lamulo loletsa kulambira mafano. (Eks 20:3-5) Yehova atamuuza kuti abwerere ku Beteli, iye anauza anthu onse amene anali naye kuti achotse mafano awo. Ndiyeno Yakobo anawononga mafano onse kuphatikizaponso ndolo zomwe anthu ankavala ngati zithumwa. (Ge 35:1-4) N’zoonekeratu kuti Yehova anasangalala ndi zimene Yakobo anachitazi.

Kodi masiku ano tingasonyeze bwanji kuti timalambira Yehova yekha? Tiyenera kupewa chilichonse chokhudzana ndi kulambira mafano kapena kukhulupirira mizimu. Zimenezi zikuphatikizapo kuchotsa chilichonse chokhudzana ndi matsenga komanso kukhala osamala ndi zosangalatsa zomwe timakonda. Mwachitsanzo, mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimakonda mabuku komanso mafilimu onena za mavampaya, mizukwa kapena zinthu zina zamatsenga? Kodi zosangalatsa zomwe ndimakonda zimandichititsa kuganiza kuti nkhani zamatsenga, kulodzana kapena kutemberera ena zilibe vuto?’ Tiyenera kupeweratu chilichonse chimene Yehova amadana nacho.​—Sl 97:10.

ONERANI VIDIYO YAKUTI “TSUTSANI MDYEREKEZI,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Palesa anakumana ndi vuto lotani?

  • N’chifukwa chiyani ndi nzeru kupempha thandizo kwa akulu ngati ifeyo, munthu amene timaphunzira naye Baibulo kapenanso munthu amene tikumudziwa akuvutitsidwa ndi ziwanda?

  • Tsutsani Mdyerekezi ndipo yandikirani Mulungu.​—Yak 4:7, 8

    Kodi ndi zinthu ziti zomwe anthu amene akufuna kuti Yehova aziwateteza ayenera kupewa?

  • Kodi Palesa anachita chiyani atathandizidwa ndi akulu?

  • Kodi m’dera limene mukukhala, ndi zinthu ziti zimene muyenera kupewa kuti musamavutitsidwe ndi ziwanda?