Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tinganene

Zimene Tinganene

●○○ ULENDO WOYAMBA

Funso: Kodi cholinga cha Mulungu polenga anthu chinali chotani?

Lemba: Ge 1:28

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi timadziwa bwanji kuti cholinga chomwe Mulungu analengera anthu chidzakwaniritsidwa?

○●○ ULENDO WOBWEREZA WOYAMBA

Funso: Kodi timadziwa bwanji kuti cholinga chomwe Mulungu analengera anthu chidzakwaniritsidwa?

Lemba: Yes 55:11

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi moyo udzakhala wotani Mulungu akadzakwaniritsa cholinga chimene analengera anthu?

○○● ULENDO WOBWEREZA WACHIWIRI

Funso: Kodi moyo udzakhala wotani Mulungu akadzakwaniritsa cholinga chomwe analengera anthu?

Lemba: Sl 37:10, 11

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi tingatani kuti tidzalandire madalitso amene Mulungu analonjeza?

NTCHITO YOITANIRA ANTHU KU CHIKUMBUTSO (March 14–April 7):

“Tikukuitanirani ku mwambo wofunika kwambiri womwe udzachitike padziko lonse. Mwambo umenewu ndi wokumbukira imfa ya Yesu.” Kenako m’patseni kapepala. “Kapepalaka kakusonyeza nthawi komanso malo omwe mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino. Tikukuitananinso kuti mudzamvetsere nkhani yapadera yomwe idzakambidwe ­kumapeto a mlungu wa March 30.”

Funso la Ulendo Wotsatira Ngati Munthuyo Wasonyeza Chidwi: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?