August 1-7
MASALIMO 87-91
Nyimbo Na. 49 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Pitirizani Kukhala M’malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba”: (10 min.)
Sal. 91:1, 2—Timatetezeka mwauzimu tikakhala “m’malo achitetezo” a Yehova (w10 2/15 26-27 ndime 10-11)
Sal. 91:3—“Wosaka mbalame” akufunitsitsa kutigwira (w07 10/1 26-30 ndime 1-18)
Sal. 91:9-14—Yehova ndi pothawirapo pathu (w10 1/15 10-11 ndime 13-14; w01 11/15 19-20 ndime 13-19)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Sal. 89:34-37—Kodi ndi pangano liti limene lafotokozedwa palembali? Nanga kodi Yehova anagwiritsa ntchito chitsanzo chotani pofuna kusonyeza kuti panganoli ndi lodalirika? (w14 10/15 10 ndime 14; w07 7/15 32 ndime 3-4)
Sal. 90:10, 12—Kodi ‘tingawerengere bwanji masiku athu kuti tikhale ndi mtima wanzeru’? (w06 7/15 13 ndime 4; w01 11/15 13 ndime 19)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 90:1-17
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Nkhani yokambirana. Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo. Limbikitsani ofalitsa kuti alembe ulaliki wawowawo.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zofunika pampingo: (5 min.)
“Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizithandiza Ophunzira Baibulo Athu Kuti Adzipereke Komanso Kubatizidwa”: (10 min.) Nkhani yokambirana. Pogwiritsa ntchito mafunso otsatirawa, funsani wofalitsa amene anathandiza munthu amene ankaphunzira naye Baibulo kuti adzipereke komanso kubatizidwa. Kodi munamuthandiza bwanji munthuyo kuti azikonda kwambiri Yehova? Nanga munamuthandiza bwanji kukwaniritsa zolinga zake?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 3 ndime 14-21, ndi bokosi patsamba 30 komanso Mfundo Zofunika Kuganizira patsamba 32.
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 137 ndi Pemphero