August 29–September 4
MASALIMO 110-118
Nyimbo Na. 61 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Yehova Ndidzamubwezera Chiyani?”: (10 min.)
Sal. 116:3, 4, 8—Yehova anathandiza wolemba Masalimo kuti asaphedwe (w87-E 3/15 24 ndime 5; w09 7/15 29 ndime 4 )
Sal. 116:12—Wolemba Masalimo anatsimikiza mtima kumuthokoza Yehova chifukwa cha zimene anamuchitira (w09 7/15 29 ndime 4-5; w98 12/1 24 ndime 3)
Sal. 116:13, 14, 17, 18—Wolemba Masalimoyu ankayesetsa kuchita zonse zimene Mulungu amafuna komanso kukwaniritsa zinthu zonse zimene anamulonjeza (w10 4/15 27, komanso bokosi)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Sal. 110:4—Kodi palembali mawu akuti ‘kulumbira’ akutanthauza chiyani? (w14 10/15 11 ndime 15-17; w06 9/1 14 ndime 1)
Sal. 116:15—Pokamba nkhani ya maliro, n’chifukwa chiyani vesili siliyenera kugwiritsidwa ntchito ponena za munthu amene wamwalirayo? (w12 5/15 22 ndime 2)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 110:1–111:10
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) ll 16—Siyani funso loti mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) ll 17—Siyani funso loti mudzakambirane ulendo wotsatira.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bh 179-181 ndime 17-19—Muthandizeni wophunzirayo kuti aone mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’ndimezi.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 82
“Kuphunzitsa Choonadi”: (7 min.) Nkhani yokambirana.
“Tidzagwira Ntchito Yapadera Yogawira Nsanja ya Olonda mu September”: (8 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo yosonyeza chitsanzo choyamba chogawira magazini m’mwezi wa September ndipo kenako kambiranani zomwe mwaona m’vidiyoyo. Limbikitsani anthu kuti adzagwire nawo ntchitoyi komanso kuti adzachite nawo upainiya wothandiza.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 5 ndime 14-26, komanso Mfundo Zofunika Kuziganizira patsamba 50.
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 144 ndi Pemphero
Kumbukirani kuti, muyenera kuika nyimboyi kuti onse aimvetsere kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo.