MOYO WATHU WA CHIKHRISTU
Kuphunzitsa Choonadi
Kuyambira m’mwezi wa September, Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu izidzakhala ndi chitsanzo cha mmene tingalalikirire cha mutu wakuti, “Kuphunzitsa Choonadi.” Cholinga cha chitsanzochi ndi kutithandiza kuti tizifotokoza mfundo inayake ya m’Baibulo pogwiritsa ntchito funso komanso lemba.
Tikaona kuti munthu ali ndi chidwi, tikhoza kumupatsa buku kapena kumuonetsa vidiyo ya pa jw.org. Tiyeni tiziyesetsa kubwerera mwachangu kwa anthu onse amene akufuna kudziwa zambiri kuti tikakambirane nawo funso limene tinawasiyira. Chitsanzo chilichonse komanso nkhani za ophunzira zizichokera m’mfundo zachidule za m’buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa. Choncho tikhozanso kuona m’bukuli kuti tidziwe mafunso ena owonjezera komanso Malemba ena oti tidzagwiritse ntchito ulendo wotsatira. M’bukuli tikhozanso kupeza Malemba oti tidzagwiritse ntchito tikamadzaphunzira ndi munthu pogwiritsa ntchito Baibulo lokha.
Pali njira imodzi yokha yopita ku moyo wosatha. (Mat. 7:13, 14) Choncho tikamalalikira anthu a zipembedzo zosiyanasiyana komanso ochokera kosiyanasiyana, tiyenera kumafotokoza mfundo za m’Baibulo m’njira yoti ziwafike pamtima kuti ayambe kuyenda panjira imeneyi. (1 Tim. 2:4) Tikayesetsa kuzolowera kumalalikira anthu pogwiritsa ntchito chitsanzochi, tidzakhala aluso kwambiri ndipo tidzakhala aphunzitsi ‘ophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.’ Zimenezi zidzachititsa kuti tizisangalala kwambiri ndipo tidzathandiza anthu ochuluka kudziwa mfundo zolondola zomwe zimapezeka m’Baibulo.—2 Tim. 2:15.