MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tidzagwira Ntchito Yapadera Yogawira Nsanja ya Olonda mu September
Anthu padzikoli akukumana ndi mavuto ambiri ndipo akufunika kuthandizidwa. (Mlal. 4:1) M’mwezi wonse wa September chaka chino, tidzagwira ntchito yapadera yogawira magazini ya Nsanja ya Olonda. Magaziniyi ili ndi nkhani zomwe zingalimbikitse anthu pa mavuto amene akukumana nawo. Tiyeni tidzayesetse kugawira anthu ambiri magazini imeneyi. Popeza tikufuna kudzalankhula ndi anthu pamaso ndi pamaso kuti tiwalimbikitse, tisadzasiye magaziniwa pakhomo lomwe sitinapeze anthu.
ZIMENE TINGANENE
Munganene kuti, “Tonse timakumana ndi mavuto ndipo timafunika kulimbikitsidwa. Koma kodi ndi ndani amene angatithandize tikakhala pamavuto? [Werengeni 2 Akorinto 1:3, 4.] Magaziniyi ikufotokoza mmene Mulungu amatithandizira tikamakumana ndi mavuto.”
Ngati munthuyo akusonyeza kuti akufuna kudziwa zambiri, m’patseni magaziniyo ndipo kenako, . . .
MUONETSENI VIDIYO YAKUTI N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPHUNZIRA BAIBULO?
Kenako m’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo.
MUFUNSENI FUNSO LIMENE MUDZAKAMBIRANE PA ULENDO WOTSATIRA
Mwachitsanzo mungamufunse kuti, “N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika?”