Akudziwitsa anthu za jw.org mumzinda wa São Paulo ku Brazil

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU August 2018

Zimene Tinganene

Zimene tinganene zofotokoza kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandizabe masiku ano.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muzisonyeza Kuyamikira

Anthu amene amafuna kusangalatsa Khristu amayesetsa kukonda komanso kuyamikira anthu onse, mosasamala kanthu kuti ndi osiyana nawo mtundu kapena chipembedzo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kumbukirani Mkazi wa Loti

Kodi tingatani kuti tipewe zimene mkazi wa Loti anakumana nazo? Nanga kodi tingatani ngati tikuona kuti kufunafuna chuma kwayamba kutilepheretsa kuchita zinthu zokhudza kulambira?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Zomwe Tikuphunzira M’fanizo la Ndalama 10 za Mina

Kodi zinthu zotsatirazi zimaimira chiyani m’fanizo la Yesu la ndalama 10 za mina: Mbuye, akapolo komanso ndalama?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Yesetsani Kudziwa Bwino Webusaiti Yathu ya JW.ORG

Mabuku komanso zinthu zina zimene zili m’gulu la Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa, zimatchula za webusaiti yathu ya jw.org. Choncho ngati titaidziwa bwino webusaiti yathuyi, ikhoza kutithandiza kwambiri tikamalalikira.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”

Posachedwapa Yesu abwera kudzawononga oipa ndi kupulumutsa anthu okhulupirika. Tiyenera kukhala okonzeka kuti tidzapulumuke.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muzikhala Okonzeka Kukhululuka

Yehova ndi Mwana wake amaona mmene mtima wa munthu ulili kuti aone ngati wasintha n’cholinga choti amukhululukire.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Yesu Anaferanso M’bale Wakoyo

Yesu anapereka moyo wake nsembe chifukwa cha anthu ochimwa. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu, omwe nawonso ndi ochimwa ngati ife tomwe?