MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Yesetsani Kudziwa Bwino Webusaiti Yathu ya JW.ORG
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Mabuku komanso zinthu zina zimene zili m’gulu la Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa, zimatchula za webusaiti yathu ya jw.org. Ndiponso cholinga cha makadi komanso kapepala kakuti, Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo? ndi kudziwitsa anthu za webusaiti yathu. Mungathe kugwiritsa ntchito webusaitiyi pogawira munthu Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa. Tikhoza kumutumizira linki kapena chinthucho kudzera pa imelo. Zimenezi n’zothandizanso ngati tinalalikira munthu amene amalankhula chinenero china. Komanso anthu ena amatha kufunsa funso lomwe yankho lake silipezeka m’Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa, koma limapezeka m’mabuku athu ena. Choncho ngati titaidziwa bwino webusaiti yathuyi, ikhoza kutithandiza kwambiri tikamalalikira.
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
-
Gwiritsani ntchito mbali yakuti “ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA.” Ngati mwakumana ndi munthu yemwe akufuna kudziwa zambiri zokhudza mmene angalelere ana ake, pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANTHU OKWATIRANA KOMANSO MABANJA.
-
Gwiritsani ntchito mbali yakuti “MABUKU.” Ngati mukufuna kulalikira mwamwayi kusukulu ndipo mukufuna kugawira kabuku kakuti Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa, pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > MABUKU.
-
Gwiritsani ntchito mbali yakuti “ZOKHUDZA IFEYO.” Ngati mukulalikira mnzanu wakuntchito amene amafuna atadziwa zambiri zokhudza zimene mumakhulupirira, pitani pamene palembedwa kuti ZOKHUDZA IFEYO > MAFUNSO OFUNSIDWA KAWIRIKAWIRI OKHUDZA A MBONI ZA YEHOVA.
ONERANI VIDIYO YAKUTI YESETSANI KUDZIWA BWINO WEBUSAITI YATHU YA JW.ORG, KENAKO KAMBIRANANI MALO AMENE MUNGAPITE PAWEBUSAITI YATHU KUTI MUTHANDIZE ANTHU OTSATIRAWA:
-
munthu yemwe sakhulupirira zoti kuli Mulungu
-
munthu amene wakumana ndi mavuto aakulu
-
m’bale kapena mlongo amene anasiya kulalikira komanso kusonkhana
-
munthu yemwe tinamulalikira ndipo akufuna kudziwa mmene timapezera ndalama zoyendetsera ntchito yathu
-
munthu wochokera dziko lina yemwe akufuna kudziwa kumene angakapeze Nyumba ya Ufumu akabwerera kwawo