Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Yesu Anaferanso M’bale Wakoyo

Yesu Anaferanso M’bale Wakoyo

Yesu anapereka moyo wake nsembe chifukwa cha anthu ochimwa. (Aroma 5:8) Sitikukayikira kuti mumayamikira chikondi chimene Yesu anatisonyezachi. Komabe nthawi zina timafunika kuchita kudzikumbutsa kuti Yesu anaferanso abale athu. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu, omwe nawonso ndi ochimwa ngati ife tomwe? Tingachite zimenezi m’njira zitatu zotsatirazi. Choyamba, m’malo momangocheza ndi anthu okhawo amene tinazolowerana nawo, tingachite bwino kumachezanso ndi anthu amene timasiyana nawo m’zinthu zambiri. (Aroma 15:7; 2 Akor. 6:12, 13) Chachiwiri, tiyenera kupewa kuchita kapena kulankhula zinthu zomwe zingakhumudwitse ena. (Aroma 14:13-15) Ndipo chomaliza, wina akatilakwira tiyenera kumakhululuka mwansanga. (Luka 17:3, 4; 23:34) Ngati titamayesetsa kutsanzira Yesu pochita zinthu zimenezi, Yehova angadalitse mpingo wathu ndi mtendere komanso mgwirizano.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, MUZIONA ZINTHU MOYENERA NDIPO KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Miki ankaona bwanji anthu a mumpingo wake atangosamukiramo kumene?

  • Kodi n’chiyani chimene chinachititsa kuti asinthe mmene ankawaonera?

  • Kodi chitsanzo cha Yesu chinamuthandiza bwanji pa nkhaniyi? (Maliko 14:38)

  • Kodi lemba la Miyambo 19:11 lingatithandize bwanji kuti tiziona Akhristu anzathu moyenera?