December 5-11
YESAYA 1-5
Nyimbo Na. 107 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Tiyeni Tipite Kukakwera Phiri la Yehova”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo yakuti, Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yesaya.]
Yes. 2:2, 3—“Phiri la nyumba ya Yehova” limaimira kulambira koyera (ip-1 38-41 ¶6-11; 45 ¶20-21)
Yes. 2:4—Anthu olambira Yehova samenya nkhondo (ip-1 46-47 ¶24-25)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yes. 1:8, 9—Kodi mawu oti “Mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati msasa m’munda wa mpesa” akutanthauza chiyani? (w06 12/1 8 ¶5)
Yes. 1:18—Kodi Yehova ankatanthauza chiyani pouza Aisiraeli kuti “tiyeni tikambirane”? (w06 12/1 9 ¶1; it-2-E 761 ¶3)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yes. 5:1-13
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Nkhani yokambirana pogwiritsa ntchito “Zitsanzo za Ulaliki.” Pambuyo poonetsa vidiyo iliyonse ya chitsanzo cha ulaliki, kambiranani mfundo zimene tikuphunzirapo. Limbikitsani ofalitsa kuti azilemba ulaliki wawowawo.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zofunika Pampingo: (7 min.) Mukhoza kukambirana mfundo zimene tikuphunzira mu Buku Lapachaka. (yb16 32 ¶3–34 ¶1)
“Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizifika Anthu Pamtima ndi Buku Lakuti Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?”: (8 min.) Nkhani yokambirana. Limbikitsani onse amene ali ndi mbali ya Phunziro la Baibulo mwezi uno kuti agwiritse ntchito mfundo zopezeka patsamba 261-262 m’buku la Sukulu ya Utumiki.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 12 ¶13-25 komanso Mfundo Zofunika Kuziganizira patsamba 107.
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 154 ndi Pemphero
Kumbukirani: Muyenera kuika nyimboyi kuti onse amvetsere, kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo.