“Tiyeni Tipite Kukakwera Phiri la Yehova”
“M’masiku otsiriza” |
Nthawi yathu ino |
“Phiri la nyumba ya Yehova” |
Kulambira Yehova movomerezeka |
“Mitundu yonse idzakhamukira kumeneko” |
Anthu olambira Mulungu movomerezeka amakhala gulu limodzi logwirizana |
“Bwerani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova” |
Olambira oona amaitana anthu ena kuti azilambira nawo limodzi |
“Iye akatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo” |
Yehova amatiphunzitsa ndiponso kutithandiza kuyenda m’njira zake pogwiritsa ntchito Mawu ake |
“Anthuwo sadzaphunziranso nkhondo” |
Yesaya anafotokoza kuti anthu adzasula zida zankhondo kuti zikhale zolimira pofuna kusonyeza kuti anthu a Yehova azidzakhala mwamtendere. Kodi zida zimenezi zinali zotani? |
‘Malupanga akhale makasu a pulawo’ |
1 Khasu la pulawo ndi limene linkagalauza nthaka ndipo nthawi zina linkakhala lachitsulo.—1 Sam. 13:20 |
‘Mikondo ikhale zida zosadzira mitengo’ |
2 Chida chosadzira mitengo chinali chooneka ngati chikwakwa. Ankagwiritsanso ntchito chidachi posadza mpesa.—Yes. 18:5 |