Mesiya Anakwaniritsa Ulosi
Kudakali zaka zambiri kuti Yesu abadwe, Yesaya ananeneratu kuti Mesiya adzalalikira “m’chigawo cha Yorodano, ku Galileya kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina.” Yesu anakwaniritsa ulosi umenewu chifukwa analalikira uthenga wabwino m’chigawo chonse cha Galileya.—Yes. 9:1, 2.
-
Anachita chozizwitsa chake choyamba pa ukwati winawake—Yoh. 2:1-11 (ku Kana)
-
Anasankha atumwi ake—Maliko 3:13, 14 (kufupi ndi ku Kaperenao)
-
Analalikira ulaliki wake wa paphiri—Mat. 5:1–7:27 (pafupi ndi ku Kaperenao)
-
Anaukitsa mwana yekhayo wa mkazi wina wamasiye—Luka 7:11-17 (ku Naini)
-
Anaonekera kwa ophunzira ake oposa 500 pambuyo poti waukitsidwa—1 Akor. 15:6 (ku Galileya)