Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zimene Mulungu Amatiphunzitsa Zimatithandiza Kuti Tisakhale Atsankho

Zimene Mulungu Amatiphunzitsa Zimatithandiza Kuti Tisakhale Atsankho

Yehova alibe tsankho. (Mac. 10:34, 35) Iye amalola kuti anthu ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse” akhale atumiki ake. (Chiv. 7:9) Choncho, anthu amene ali mumpingo wachikhristu sayenera kuchita zinthu mwatsankho kapena mokondera. (Yak. 2:1-4) Zimene Mulungu amatiphunzitsa zatithandiza kuti tizisangalala ndi paradaiso wauzimu ndipo timaona anthu akusintha makhalidwe awo. (Yes. 11:6-9) Tikamayesetsa kuchotsa mtima watsankho, timasonyeza kuti tikutsanzira Mulungu.—Aef. 5:1, 2.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, JOHNY NDI GIDEON: ANALI KHOSWE NDI MPHAKA KOMA PANO NDI OGWIRIZANA. KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Mulungu amatiphunzitsa ndi zimene zingathandize kwambiri pothetsa tsankho kuposa zimene anthu paokha amachita?

  • N’chiyani chimakuchititsani chidwi mukaona mgwirizano umene ulipo pakati pa abale ndi alongo padziko lonse?

  • Kodi Yehova amalemekezedwa bwanji tikamayesetsa kukhalabe ogwirizana monga Akhristu?