December 26– January 1
YESAYA 17-23
Nyimbo Na. 123 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Munthu Akamagwiritsa Ntchito Udindo Wake Molakwika Amachotsedwa pa Udindowo”: (10 min.)
Yes. 22:15, 16—Sebina anagwiritsa ntchito udindo wake mongofuna kudzipindulitsa yekha (ip-1 238-239 ¶16-17)
Yes. 22:17-22—Yehova anachotsa Sebina pa udindo n’kuikapo Eliyakimu (ip-1 238-240 ¶17-18)
Yes. 22:23-25—Tingaphunzire zambiri pa zimene zinachitikira Sebina (w07 1/15 9 ¶1; ip-1 240-241 ¶19-20)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yes. 21:1—Kodi ndi dera liti lomwe ankalitchula kuti “chipululu cha nyanja,” ndipo n’chifukwa chiyani? (w06 12/1 11 ¶2)
Yes. 23:17, 18—Kodi phindu ndi malipiro a mzinda wa Turo zinakhala bwanji zinthu “zopatulika kwa Yehova”? (ip-1 253-254 ¶22-24)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yes. 17:1-14
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) bhs–
Gwiritsani ntchito vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo kuti mugawire bukuli. (Dziwani izi: Musaonetse vidiyoyi m’chitsanzochi.) Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) bhs–
Yambitsani phunziro la Baibulo lachidule ndipo muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira. Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) lv 151 ¶10-11–
Sonyezani mmene tingafikire pamtima wophunzira wathu.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 44
Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?: (8 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2015, tsamba 12-16. Limbikitsani onse kuti apitirize kukhala maso mofanana ndi mlonda amene Yesaya anatchula komanso anamwali 5 ochenjera a m’fanizo la Yesu.—Yes. 21:8; Mat. 25:1-13.
Zimene Gulu Lathu Lachita: (7 min.) Onetsani vidiyo yakuti, Zimene Gulu Lathu Lachita ya December.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 14 ¶1-13.
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 141 ndi Pemphero