Munthu Akamagwiritsa Ntchito Udindo Wake Molakwika Amachotsedwa pa Udindowo
Sebina anali “kapitawo woyang’anira nyumba ya mfumu,” ndipo n’kutheka kuti inali nyumba ya Mfumu Hezekiya. Pa udindo umenewu, iye anali wachiwiri kwa mfumu ndipo ankayenera kuthandiza Aisiraeli.
-
Sebina ankayenera kusamalira zimene anthu a Yehova ankafunikira
-
Iye anasonyeza kudzikonda chifukwa anachita zinthu zongofuna kuti atchuke
-
Yehova anachotsa Sebina pa udindo wake n’kuikapo Eliyakimu
-
Eliyakimu anapatsidwa “makiyi a nyumba ya Davide,” zomwe zikuimira mphamvu komanso ulamuliro
Taganizirani izi: Kodi Sebina akanagwiritsa ntchito bwanji udindo wake kuti athandize anthu ena?