Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzithandiza Anthu Amene Ali ndi “Maganizo Abwino” Kuti Akhale Ophunzira

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzithandiza Anthu Amene Ali ndi “Maganizo Abwino” Kuti Akhale Ophunzira

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Yehova amachititsa kuti mbewu za choonadi zikule m’mitima mwa anthu omwe ali ndi ‘maganizo abwino amene angawathandize kudzapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48; 1 Akor. 3:7) Timagwira ntchito limodzi ndi Yehova tikamayesetsa kuchita khama kuthandiza anthu omwe angamvetsere uthenga wathu. (1 Akor. 9:26) Anthuwa ayenera kudziwa kuti ubatizo wachikhristu ndi wofunika kwambiri kuti adzapulumuke. (1 Pet. 3:21) Timathandiza anthu omwe timaphunzira nawo Baibulo kuti asinthe moyo wawo, azilalikira ndi kuphunzitsa ndiponso kuti adzipereke kwa Yehova.​—Mat. 28:19, 20.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Muzikumbutsa anthu amene mumaphunzira nawo Baibulo kuti cholinga cha phunzirolo ndi kuwathandiza “kudziwa” Yehova ndiponso kuti azichita zimene iye amafuna.​—Yoh. 17:3

  • Muziwathandiza kulimbana ndi mavuto omwe amakumana nawo pa moyo wawo, monga kusiya makhalidwe oipa komanso kusiya kucheza ndi anthu oipa

  • Muziwalimbikitsa komanso kuwathandiza kuti akhalebe olimba asanabatizidwe komanso akabatizidwa.​—Mac. 14:22

ONERANI VIDIYO YAKUTI, YEHOVA MULUNGU ADZAKUTHANDIZANI, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingachititse kuti munthu azichita mantha kudzipereka komanso kubatizidwa?

  • Kodi akulu angathandize bwanji anthu amene akuphunzira Baibulo kuti apite patsogolo mwauzimu?

  • Kodi lemba la Yesaya 41:10, limatiphunzitsa chiyani ponena za Yehova?

  • Kodi ndi makhalidwe ati omwe angatithandize kuti tizitumikira Yehova m’njira yoyenera ngakhale kuti ndife ochimwa?

Kodi timagwira bwanji ntchito ndi Yehova tikamapanga ophunzira?