Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mpingo ukumvetsera malangizo ochokera ku bungwe lolamulira

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 15-16

Anasankha Zochita Pogwiritsa Ntchito Mawu a Mulungu

Anasankha Zochita Pogwiritsa Ntchito Mawu a Mulungu

Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yokhudza mmene nkhani yamdulidwe inathetsedwera?

15:1, 2—Tizikhala odzichepetsa komanso oleza mtima. M’malo mothetsa nkhaniyi okha, Paulo ndi Baranaba anapempha malangizo kuchokera ku gulu la Yehova.

15:28, 29—Tizidalira gulu la Yehova. Mpingo unkakhulupirira kuti Yehova apitiriza kuutsogolera pogwiritsa ntchito mzimu woyera komanso Khristu Yesu.

16:4, 5—Tizikhala omvera. Mipingo inapitiriza kukulirakulira pamene inkatsatira malangizo ochokera ku bungwe lolamulira.