Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizitamanda Yehova Mosangalala Poimba Nyimbo

Tizitamanda Yehova Mosangalala Poimba Nyimbo

Paulo ndi Sila ali m’ndende, anatamanda Yehova poimba nyimbo. (Mac. 16:25) Sitikukayikira kuti nyimbo zimene anaimba zinawathandiza kuti apitirize kupirira. Nanga bwanji masiku ano? Nyimbo zimene timaimba polambira komanso nyimbo zina zomwe zimaimbidwa ndi gulu lathu, zimatilimbikitsa komanso kutithandiza kuti tikhalebe okhulupirika tikakumana ndi mayesero. Kuposa pamenepo, nyimbozi zimatamanda Yehova. (Sal. 28:7) Timalimbikitsidwa kuti tiziyesetsa kuloweza mawu a zina mwa nyimbozi. Kodi inuyo munayesapo kuchita zimenezi? Tikhoza kumagwiritsa ntchito nthawi ya kulambira kwa pabanja kuti tiphunzire komanso kuloweza mawu a nyimbo zathu.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ANA ANATAMANDA YEHOVA POIMBA NYIMBO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi kuimba nyimbo za Ufumu kungatithandize bwanji?

  • Kodi a m’dipatimenti yojambula amakonzekera bwanji akamafuna kujambula nyimbo?

  • Kodi ana komanso makolo awo amakonzekera bwanji nthawi yojambula nyimbo isanafike?

  • Kodi ndi nyimbo za Ufumu ziti zimene inuyo mumakonda, nanga n’chifukwa chiyani mumazikonda?