Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 9-11

Munthu Amene Ankazunza Akhristu Anakhala Mkhristu Wakhama

Munthu Amene Ankazunza Akhristu Anakhala Mkhristu Wakhama

9:15, 16, 20-22

Saulo sanachedwe kukhala Mkhristu mogwirizana ndi zimene ankaphunzira. N’chiyani chinathandiza Saulo kusintha mwachangu chonchi pomwe ena zinkawavuta? Chifukwa choti ankaopa kwambiri Mulungu osati anthu ndiponso ankayamikira chifundo chimene Khristu anamusonyeza. Ngati mukuphunzira Baibulo koma simunabatizidwe, kodi mungakonde kutsanzira Saulo n’kuyamba kuchita mogwirizana ndi zimene mwaphunzira?